Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 13 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 A wise son heeds his father's instruction, but a scoffer does not listen to rebuke. Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake, koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.
2 From the fruit of his mouth a person enjoys good things, but the appetite of the treacherous is for violence. Munthu amapeza zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake, koma anthu osakhulupirika amalakalaka zachiwawa basi.
3 Whoever guards his mouth protects his life, but one who opens his lips wide comes to ruin. Iye amene amagwira pakamwa pake amateteza moyo wake, koma amene amayankhula zopanda pake adzawonongeka.
4 The lazy person craves and gets nothing, but the appetite of the diligent is richly satisfied. Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, koma munthu wakhama adzalemera.
5 The righteous hates falsehood, but the wicked brings shame and disgrace. Munthu wolungama amadana ndi zabodza, koma zochita za munthu woyipa zimanyansa ndiponso zimachititsa manyazi.
6 Righteousness guards the one whose way is blameless, but wickedness overthrows the sinner. Chilungamo chimateteza munthu wangwiro, koma tchimo limagwetsa munthu wochimwa.
7 One person pretends to be rich, yet has nothing; another pretends to be poor, yet has great wealth. Wina amadziyesa kuti ndi wolemera chonsecho alibe kanthu kalikonse; munthu wina amaoneka ngati wosauka chonsecho ali ndi chuma chambiri.
8 A person's wealth may ransom his life, but the poor hears no threat. Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake, koma munthu wosauka amamva chidzudzulo.
9 The light of the righteous shines joyfully, but the lamp of the wicked will be snuffed out. Nyale ya munthu wolungama ndi yokondweretsa, koma nyale ya munthu woyipa imazimitsidwa.
10 Arrogance breeds nothing but strife, but wisdom is with those who seek advice. Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano, koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru.
11 Wealth gained by fraud dwindles away, but whoever gathers little by little makes it grow. Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira.
12 Hope deferred makes the heart sick, but desire fulfilled is a tree of life. Chinthu chochiyembekezera chikalephereka chimalefula mtima, koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi chimakhala ngati mtengo wamoyo.
13 Whoever despises the word brings ruin on himself, but the one who reveres the commandment will be rewarded. Amene amanyoza malangizo adzawonongeka, koma amene amasamala lamulo amalandira mphotho.
14 The teaching of the wise is a fountain of life, turning a person away from the snares of death. Malangizo a munthu wanzeru ali ngati kasupe wamoyo; amathandiza munthu kuti asakondwe mu msampha wa imfa.
15 Good sense wins favor, but the way of the treacherous is their undoing. Munthu wa nzeru zabwino amapeza kuyanja pakati pa anthu, koma munthu wosakhulupirika adzawonongeka.
16 Every prudent person acts with knowledge, but a fool flaunts his foolishness. Munthu wochenjera amachita zinthu mwanzeru, koma chitsiru chimaonetsa poyera uchitsiru wake.
17 A wicked messenger falls into trouble, but a faithful envoy brings healing. Wamthenga woyipa amagwetsa anthu mʼmavuto, koma nthumwi yodalirika imabweretsa mtendere.
18 Poverty and shame come to whoever ignores discipline, but the one who heeds correction is honored. Wokana mwambo adzasauka ndi kunyozedwa, koma wosamala chidzudzulo adzalemekezedwa.
19 A desire fulfilled is sweet to the soul, but turning away from evil is detestable to fools. Chinthu chochilakalaka chikachitika chimasangalatsa mtima, koma zitsiru zimadana ndi kuleka zoyipa.
20 Whoever walks with the wise grows wise, but the companion of fools suffers harm. Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru; koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.
21 Disaster pursues sinners, but good rewards the righteous. Choyipa chitsata mwini, koma wochita zolungama adzalandira mphotho yabwino.
22 A good person leaves an inheritance to his grandchildren, but the sinner's wealth is stored up for the righteous. Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake cholowa, koma chuma cha munthu wochimwa amachilandira ndi olungama.
23 The unplowed field of the poor could yield abundant food, but it is swept away for lack of justice. Tsala la munthu wosauka limalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amachilanda.
24 Whoever withholds the rod hates his son, but the one who loves him is diligent to discipline him. Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda, koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.
25 The righteous eats to his heart's content, but the belly of the wicked goes hungry. Munthu wolungama amakhala ndi zakudya zoti adye nʼkukhuta, koma mʼmimba mwa munthu woyipa mumakhala pululu ndi njala.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]