Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 12 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Whoever loves discipline loves knowledge, but whoever hates correction is senseless. Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu, koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.
2 A good man obtains favor from our Father, but he condemns the man who schemes evil. Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Yehova, koma Yehova amatsutsa munthu wochita chinyengo.
3 No one is established by wickedness, but the root of the righteous will never be moved. Munthu sangakhazikike bwino pochita zoyipa, koma maziko a anthu olungama sadzatekeseka.
4 A wife of noble character is her husband's crown, but one who brings shame is like decay in his bones. Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
5 The plans of the righteous are just, but the advice of the wicked is deceitful. Maganizo a anthu olungama ndi owongoka, koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo.
6 The words of the wicked lie in wait for blood, but the speech of the upright rescues the innocent. Mawu a anthu oyipa ndi ophetsa, koma mawu a anthu olungama amapulumutsa.
7 The wicked are overthrown and are no more, but the house of the righteous will stand. Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika, koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.
8 A person is praised according to their good sense, but one with a warped mind is despised. Munthu amatamandidwa malinga ndi nzeru zake, koma anthu amitima yokhota amanyozedwa.
9 Better to be lowly and have a servant than to pretend to greatness and go hungry. Nʼkwabwino kukhala munthu wonyozeka koma wodzigwirira ntchito nʼkukhala ndi zonse zofunika, kuposa kukhala wodzikuza koma ulibe ndi chakudya chomwe.
10 The righteous care for the needs of their animals, but even the mercy of the wicked is cruel. Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake, koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.
11 Whoever works their land will have plenty of food, but whoever chases worthless pursuits lacks sense. Wolima mʼmunda mwake mwakhama adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma wotsata zopanda pake alibe nzeru.
12 The wicked crave the plunder of evil men, but the root of the righteous yields fruit. Munthu woyipa amalakalaka zofunkha za anthu oyipa, koma mizu ya anthu olungama imabereka zipatso.
13 An evil man is trapped by his sinful talk, but the righteous escapes from trouble. Munthu woyipa amakodwa mu msampha wa mayankhulidwe ake oyipa; koma munthu wolungama amatuluka mʼmavuto.
14 From the fruit of their words a person is filled with good things, and the work of their hands comes back to reward them. Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.
15 The way of a fool seems right in his own eyes, but the wise listen to advice. Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino, koma munthu wanzeru amamvera malangizo.
16 A fool shows his anger at once, but the prudent overlook an insult. Mkwiyo wa chitsiru umadziwika nthawi yomweyo, koma munthu wanzeru sasamala kunyozedwa.
17 Whoever speaks the truth gives honest testimony, but a false witness tells lies. Woyankhula zoona amapereka umboni woona, koma mboni yabodza imafotokoza zonama.
18 Reckless words pierce like a sword, but the tongue of the wise brings healing. Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga, koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.
19 Truthful lips endure forever, but a lying tongue lasts only a moment. Mawu woona amakhala mpaka muyaya koma mawu abodza sakhalitsa.
20 Deceit fills the hearts of those who plot evil, but joy belongs to those who promote peace. Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo; koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe.
21 No harm overtakes the righteous, but the wicked are full of trouble. Palibe choyipa chimene chimagwera munthu wolungama, koma munthu woyipa mavuto samuthera.
22 Lying lips are detestable to our Father, but those who act faithfully are his delight. Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.
23 The prudent keep their knowledge to themselves, but the heart of fools blurts out foolishness. Munthu wochenjera amabisa nzeru zake, koma munthu wopusa amaonetsa uchitsiru wake poyera.
24 Diligent hands will rule, but laziness ends in forced labor. Ogwira ntchito mwakhama adzalamulira, koma aulesi adzakhala ngati kapolo.
25 Anxiety weighs down the heart, but a kind word cheers it up. Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu, koma mawu abwino amamusangalatsa.
26 The righteous guide their neighbor, but the way of the wicked leads them astray. Munthu wolungama amatsogolera mnansi wake, koma ntchito za anthu oyipa zimawasocheretsa.
27 The lazy do not roast their game, but the diligent prize their possessions. Munthu waulesi sapeza chimene akufuna, koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengo wapatali.
28 In the path of righteousness there is life, and along that way there is no death. Mʼnjira yachilungamo muli moyo; koma njira ya munthu woyipa imafikitsa ku imfa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]