Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 11 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Dishonest scales are an abomination to our Father, but accurate weights are his delight. Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.
2 When pride comes, then comes disgrace, but wisdom comes with the humble. Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.
3 The integrity of the upright guides them, but the crookedness of the treacherous destroys them. Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.
4 Wealth does not profit in the day of wrath, but righteousness delivers from death. Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
5 The righteousness of the blameless makes their way straight, but the wicked falls by his own wickedness. Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo, koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo.
6 The righteousness of the upright delivers them, but the treacherous are trapped by their own craving. Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa, koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.
7 When a wicked person dies, his hope perishes, and his confidence in his own strength comes to nothing. Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso. Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka.
8 The righteous is delivered from trouble, and the wicked comes into it in his place. Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto, koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa.
9 With his mouth the godless destroys his neighbor, but through knowledge the righteous are delivered. Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake, koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu.
10 When things go well for the righteous, the city rejoices, and when the wicked perish, there are shouts of joy. Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera, ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.
11 By the blessing of the upright a city is exalted, but by the mouth of the wicked it is torn down. Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima, koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa.
12 Whoever despises his neighbor lacks sense, but a person of understanding stays silent. Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru, koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete.
13 A gossip goes about revealing secrets, but someone with a trustworthy spirit can keep a secret. Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi; koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.
14 Where there is no guidance, a people falls, but in an abundance of counselors there is safety. Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa; koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.
15 Whoever puts up security for a stranger will surely suffer for it, but whoever hates shaking hands on a pledge is secure. Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto, koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere.
16 A gracious woman attains honor, and ruthless men attain riches. Mkazi wodekha amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma.
17 A kind person benefits himself, but a cruel person brings trouble on himself. Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.
18 The wicked earns deceptive wages, but whoever sows righteousness earns a true reward. Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu, koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni.
19 Whoever is steadfast in righteousness finds life, but whoever pursues evil runs to his own death. Munthu wochita za chilungamo amapeza moyo, koma wothamangira zoyipa adzafa.
20 Those of crooked heart are an abomination to our Father, but those whose ways are blameless are his delight. Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhota koma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro.
21 You can be sure the evil person will not go unpunished, but the children of the righteous will go free. Zoonadi, anthu oyipa adzalangidwa, koma anthu olungama adzapulumuka.
22 Like a gold ring in a pig's snout is a beautiful woman who shows no discretion. Monga imaonekera mphete yagolide ikakhala pa mphuno ya nkhumba, ndi momwenso amaonekera mkazi wokongola wamʼkamwa.
23 The desire of the righteous ends only in good, but the hope of the wicked ends in wrath. Zokhumba za anthu olungama zimathera pa zabwino zokhazokha, koma chiyembekezo cha anthu oyipa chimathera mu ukali wa Mulungu.
24 One person gives freely, yet grows all the richer; another withholds what is right, only to end up in need. Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe; wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe.
25 A generous soul will be enriched, and whoever refreshes others will himself be refreshed. Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera; iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa.
26 The people curse whoever holds back grain, but the one who sells it is blessed. Anthu amatemberera womana anzake chakudya, koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho.
27 Whoever diligently seeks good seeks favor, but whoever searches for evil, evil will come to him. Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo, koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza.
28 Whoever trusts in his riches will fall, but the righteous will flourish like green leaves. Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota, koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.
29 Whoever brings trouble on his own household will inherit the wind, and the fool will be servant to the wise of heart. Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto, ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.
30 The fruit of the righteous is a tree of life, and whoever wins souls is wise. Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo, ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.
31 If the righteous is repaid on earth, how much more the wicked and the sinner! Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi, kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]