Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 10 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The proverbs of Solomon: A wise son brings joy to his father, but a foolish son brings grief to his mother. Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.
2 Treasures gained by wickedness do not profit, but righteousness rescues from death. Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
3 Our Father will not let the righteous go hungry, but he thwarts the craving of the wicked. Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala; koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.
4 Lazy hands make you poor, but diligent hands bring wealth. Wochita zinthu mwaulesi amasauka, koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.
5 He who gathers in summer is a prudent son, but he who sleeps during harvest is a son who brings shame. Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru, koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.
6 Blessings rest on the head of the righteous, but the mouth of the wicked conceals violence. Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama, koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.
7 The memory of the righteous is a blessing, but the name of the wicked will rot. Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso, koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.
8 A wise heart accepts commands, but a babbling fool comes to ruin. Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.
9 Whoever walks in integrity walks securely, but he who makes his ways crooked will be found out. Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
10 Whoever winks causes trouble, and a babbling fool comes to ruin. Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto, koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.
11 The mouth of the righteous is a fountain of life, but the mouth of the wicked conceals violence. Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo, koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.
12 Hatred stirs up conflict, but love covers all offenses. Udani umawutsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.
13 On the lips of the discerning, wisdom is found, but a rod is for the back of one who lacks sense. Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu, koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.
14 The wise store up knowledge, but the mouth of a fool invites ruin. Anzeru amasunga chidziwitso koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.
15 The wealth of the rich is their fortified city; the ruin of the poor is their poverty. Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.
16 The wage of the righteous leads to life; the gain of the wicked leads to sin. Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama, koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.
17 Whoever accepts discipline is on the path to life, but he who ignores correction leads others astray. Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo, koma wonyoza chidzudzulo amasochera.
18 Whoever conceals hatred is a liar, and whoever spreads slander is a fool. Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.
19 Where words are many, sin is never absent; but whoever holds his tongue is wise. Mawu akachuluka zolakwa sizisowa, koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.
20 The tongue of the righteous is choice silver; the heart of the wicked is worth little. Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.
21 The lips of the righteous nourish many, but fools die for lack of sense. Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri; koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.
22 The blessing of our Father brings wealth, and he adds no sorrow with it. Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
23 Doing wickedness is a game to a fool, but wisdom is the delight of a person of understanding. Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa, koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.
24 What the wicked dreads will come upon him, but the desire of the righteous will be granted. Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira; chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.
25 When the storm has passed, the wicked are gone, but the righteous are established forever. Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa, koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.
26 Like vinegar to the teeth and smoke to the eyes, so is the sluggard to those who send him. Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso, ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.
27 The fear of our Father lengthens life, but the years of the wicked will be cut short. Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo; koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.
28 The hope of the righteous brings joy, but the expectation of the wicked will perish. Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe, koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.
29 The way of our Father is a refuge for the blameless, but ruin for those who do evil. Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino, koma wochita zoyipa adzawonongeka.
30 The righteous will never be shaken, but the wicked will not remain in the land. Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.
31 The mouth of the righteous yields wisdom, but the perverse tongue will be cut off. Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru, koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32 The lips of the righteous know what is acceptable, but the mouth of the wicked, only what is perverse. Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula, koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]