Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 9 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Wisdom has built her house; she has hewn out her seven pillars. Nzeru inamanga nyumba yake; inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.
2 She has slaughtered her animals; she has mixed her wine; she has also set her table. Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake; inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.
3 She has sent out her young women to call from the highest places of the town: Nzeruyo inatuma adzakazi ake, kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,
4 "Whoever is simple, let him come in here!" To the one who lacks sense she says, “Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!” Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,
5 "Come, eat my bread and drink the wine I have mixed. “Bwerani, dzadyeni chakudya changa ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.
6 Leave your simple ways, and live; walk in the way of insight." Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo; yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”
7 Whoever corrects a mocker brings abuse on himself, and whoever rebukes a wicked man gets hurt. Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo; aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.
8 Do not rebuke a mocker, or he will hate you; rebuke a wise man, and he will love you. Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe; dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.
9 Instruct a wise man and he will grow wiser; teach a righteous man and he will learn even more. Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru; ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.
10 The fear of our Father is the beginning of wisdom, and the knowledge of the Holy One is insight. Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
11 For by me your days will be multiplied, and years will be added to your life. Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.
12 If you are wise, you are wise for yourself; if you scoff, you alone will bear it. Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa; ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.
13 The woman Folly is loud; she is naive and knows nothing. Uchitsiru ndi mkazi waphokoso, wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.
14 She sits at the door of her house, on a seat at the highest places of the town, Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake, pamalo aatali a mu mzinda,
15 calling to those who pass by, who are going straight on their way: kuti aziyitana anthu ongodutsa, amene akunka nayenda njira zawo.
16 "Whoever is simple, let him come in here!" And to the one who lacks sense she says, Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,” ndipo kwa wopanda nzeru amati,
17 "Stolen water is sweet, and bread eaten in secret is pleasant." “Madzi akuba ndiye amatsekemera; chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”
18 But he does not know that the dead are there, that her guests are in the depths of the grave. Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko, ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]