Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 8 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Does not Wisdom call out, and understanding raise her voice? Kodi nzeru sikuyitana? Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?
2 Atop the heights along the way, where the paths meet, she takes her stand. Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira, imayima pa mphambano ya misewu.
3 Beside the gates, at the entrance to the city, at the doorways she cries aloud: Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda, pa makomo olowera imafuwula kuti,
4 "To you, all people, I call out; my voice reaches all humanity. Inu anthu, ndikuyitana inu; ndikuyitanatu anthu onse.
5 You who are simple, learn prudence; you who are foolish, gain an understanding heart. Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera; inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.
6 Listen, for I speak of noble things, and everything I say is right. Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri; ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama.
7 My mouth utters truth, for my lips detest wickedness. Pakamwa panga pamayankhula zoona ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.
8 All the words of my mouth are righteous; none of them is twisted or crooked. Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama; mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka.
9 To the one who understands they are all clear, and right to those who find knowledge. Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona; kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza.
10 Take my instruction instead of silver, and knowledge rather than choice gold, Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva, nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino.
11 for wisdom is better than jewels, and nothing you desire can compare with her. Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali, ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.
12 I, Wisdom, dwell with prudence, and I find knowledge and discretion. Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera. Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino.
13 The fear of our Father is to hate evil. Pride and arrogance, the evil way, and perverse speech I hate. Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.
14 Counsel is mine, and sound wisdom; I am understanding; strength is mine. Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino; ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu.
15 By me kings reign, and rulers decree what is just; Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira. Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama.
16 by me princes govern, and nobles—all who rule with justice. Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula. Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko.
17 I love those who love me, and those who search for me find me. Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza.
18 With me are riches and honor, enduring wealth and righteousness. Ine ndili ndi chuma ndi ulemu, chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika.
19 My fruit is better than gold, than the finest gold, and what I yield surpasses choice silver. Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri.
20 I walk in the way of righteousness, along the paths of justice, Ndimachita zinthu zolungama. Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo.
21 giving wealth as an inheritance to those who love me, and filling their treasuries. Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.
22 Our Father brought me forth at the beginning of his way, before his works of old. “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba. Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.
23 From ages past I was established, from the beginning, before the earth began. Ndinapangidwa kalekalelo, pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.
24 When there were no deep waters I was brought forth, when there were no springs overflowing with water. Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi, zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.
25 Before the mountains were settled, before the hills, I was brought forth, Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo, mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,
26 while he had not yet made the earth and its fields, or the first dust of the world. lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake; lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.
27 When he set the heavens in place, I was there; when he drew a circle over the face of the deep, Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga, pamene ankalemba malire a nyanja yozama,
28 when he set the skies in place above, when he established the springs of the deep, pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,
29 when he set for the sea its boundary so the waters would not cross their limits, when he marked out the foundations of the earth, pamene anayikira nyanja malire kuti madzi asadutse malirewo, ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.
30 then I was beside him as a master craftsman, and I was his daily delight, rejoicing before him always, Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri; ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku, kusangalala nthawi zonse pamaso pake.
31 rejoicing in his whole world, and delighting in the human family. Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”
32 And now, my children, listen to me: blessed are those who keep my ways. “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni; odala anthu amene amasunga njira zanga.
33 Listen to instruction and be wise; do not ignore it. Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru; musanyozere mawu anga.
34 Blessed is the one who listens to me, watching daily at my gates, waiting beside my doorway. Wodala munthu amene amandimvera, amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku, kudikirira pa chitseko changa.
35 For whoever finds me finds life and receives favor from our Father. Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo ndipo Yehova amamukomera mtima.
36 But whoever misses me harms his own soul; all who hate me love death." Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha; onse amene amandida amakonda imfa.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]