Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 7 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 My son, keep my words, and store up my commandments within you. Mwana wanga, mvera mawu anga; usunge bwino malamulo angawa.
2 Keep my commandments and live; guard my teaching as the apple of your eye. Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo; samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.
3 Bind them on your fingers; write them on the tablet of your heart. Uchite ngati wawamangirira pa zala zako, ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.
4 Say to wisdom, "You are my sister," and call understanding your dearest friend, Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,” ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
5 to keep you from the forbidden woman, from the stranger with her smooth words. Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo.
6 For at the window of my house I looked down through my lattice, Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga ndinasuzumira pa zenera.
7 and I saw among the naive, I noticed among the young men, a youth who lacked sense, Ndinaona pakati pa anthu opusa, pakati pa anyamata, mnyamata wina wopanda nzeru.
8 passing through the street near her corner, taking the road to her house, Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo, kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.
9 in the twilight, as the day faded, in the dark of night and gloom. Inali nthawi yachisisira madzulo, nthawi ya usiku, kuli mdima.
10 And there a woman comes to meet him, dressed like a prostitute, with cunning in her heart. Ndipo mkaziyo anadzakumana naye, atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.
11 She is loud and defiant; her feet will not stay at home. (Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve, iye ndi wosakhazikika pa khomo.
12 Now in the street, now in the squares, she lurks at every corner. Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika, ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).
13 She grabs him and kisses him, and with a brazen face she says to him: Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,
14 "I had peace offerings to bring; today I have paid my vows. “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano. Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.
15 So I came out to meet you, to look for you eagerly, and I have found you. Choncho ndinabwera kudzakumana nawe; ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!
16 I have spread my bed with coverings, with colored linens from Egypt. Pa bedi panga ndayalapo nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.
17 I have perfumed my bed with myrrh, aloes, and cinnamon. Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.
18 Come, let us drink deep of love until morning; let us lose ourselves in love. Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa; tiye tisangalatsane mwachikondi!
19 For my husband is not at home; he has gone on a long journey. Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako; wapita ulendo wautali:
20 He took a bag of money with him and will not come home until the full moon." Anatenga thumba la ndalama ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”
21 With all her persuasive words she sways him; with her smooth lips she draws him in. Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo; amukopa ndi mawu ake oshashalika.
22 All at once he follows her, like an ox going to the slaughter, like a deer stepping into a snare, Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo ngati ngʼombe yopita kukaphedwa, monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,
23 until an arrow pierces its liver; like a bird darting into a trap, he does not know it will cost him his life. mpaka muvi utalasa chiwindi chake, chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe, osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.
24 Now then, my sons, listen to me, and pay attention to what I say. Tsono ana inu, ndimvereni; mvetsetsani zimene ndikunena.
25 Do not let your heart turn aside to her ways; do not wander into her paths. Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu; musasochere potsata njira zake.
26 For she has brought down many victims; her slain are a mighty multitude. Paja iye anagwetsa anthu ambiri; wapha gulu lalikulu la anthu.
27 Her house is the road to the grave, going down to the chambers of death. Nyumba yake ndi njira yopita ku manda, yotsikira ku malo a anthu akufa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]