Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 6 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 My son, if you have put up security for your neighbor, if you have shaken hands in pledge for a stranger, Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole, ngati walonjeza kumulipirira mlendo,
2 you have been snared by the words of your mouth, caught by the words of your mouth. ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena, wakodwa ndi mawu a mʼkamwa mwako.
3 Then do this, my son, and free yourself, for you are now at your neighbor's mercy: go, humble yourself, and plead with your neighbor. Tsono popeza iwe mwana wanga wadziponya mʼmanja mwa mnansi wako, chita izi kuti udzipulumutse: pita msanga ukamupemphe mnansi wako; kuti akumasule!
4 Give no sleep to your eyes, no slumber to your eyelids. Usagone tulo, usawodzere.
5 Free yourself like a gazelle from the hand, like a bird from the hand of the trapper. Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje, ndi monga imachitira mbalame mu msampha wa munthu wosaka.
6 Go to the ant, you sluggard; consider her ways and be wise. Pita kwa nyerere, mlesi iwe; kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu!
7 Without having any chief, officer, or ruler, Zilibe mfumu, zilibe woyangʼanira kapena wolamulira,
8 she prepares her bread in summer and gathers her food in harvest. komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe ndipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola.
9 How long will you lie there, sluggard? When will you arise from your sleep? Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe? Kodi tulo tako tidzatha liti?
10 A little sleep, a little slumber, a little folding of the hands to rest, Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼono ndingopinda manjawa pangʼono kuti ndipumule,
11 and poverty will come upon you like a robber, and scarcity like an armed man. umphawi udzakugwira ngati mbala ndipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba.
12 A worthless person, a wicked man, goes about with crooked speech, Munthu wachabechabe, munthu woyipa, amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa,
13 winks with his eyes, signals with his feet, points with his fingers, amatsinzinira maso ake, namakwakwaza mapazi ake ndi kulozaloza ndi zala zake,
14 with perverted heart he devises evil, continually sowing discord; amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengo ndipo nthawi zonse amangokhalira kuyambitsa mikangano pakati pa anthu.
15 therefore calamity will come upon him suddenly; in a moment he will be broken beyond healing. Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa; adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa.
16 There are six things our Father hates, seven that are detestable to him: Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa:
17 haughty eyes, a lying tongue, and hands that shed innocent blood, maso onyada, pakamwa pabodza, manja akupha munthu wosalakwa,
18 a heart that devises wicked plans, feet that hurry to run to evil, mtima wokonzekera kuchita zoyipa, mapazi othamangira msanga ku zoyipa,
19 a false witness who breathes out lies, and one who sows discord among brothers. mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.
20 My son, keep your father's commandment, and do not forsake your mother's teaching. Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako; ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.
21 Bind them on your heart always; tie them around your neck. Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse, uzimangirire mʼkhosi mwako.
22 When you walk, they will lead you; when you lie down, they will watch over you; and when you awake, they will talk with you. Ukamayenda, zidzakulozera njira; ukugona, zidzakulondera; ukudzuka, zidzakuyankhula.
23 For the commandment is a lamp and the teaching a light, and the reproofs of discipline are the way of life, Paja malamulo awa ali ngati nyale, malangizowa ali ngati kuwunika, ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo moyo weniweni,
24 to keep you from the evil woman, from the smooth tongue of the adulteress. kukupulumutsa kwa mkazi wadama, zimenezi zidzakutchinjiriza kwa mkazi wadama, ndi kukuthandiza kuti usamvere mawu oshashalika a mkazi wachiwerewere.
25 Do not desire her beauty in your heart, and do not let her capture you with her eyelashes; Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake, asakukope ndi zikope zake,
26 for the price of a prostitute is only a loaf of bread, but a married woman hunts down a precious life. paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi ndipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse.
27 Can a man carry fire next to his chest and his clothes not be burned? Kodi munthu angathe kutenga moto zovala zake osapsa?
28 Or can one walk on hot coals and his feet not be scorched? Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto mapazi ake osapserera?
29 So is he who sleeps with his neighbor's wife; none who touches her will go unpunished. Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina. Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa.
30 People do not despise a thief if he steals to satisfy his appetite when he is hungry, Paja anthu sayinyoza mbala ikaba chifukwa chakuti ili ndi njala.
31 but if he is caught, he will pay sevenfold; he will give all the goods of his house. Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri, ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake.
32 He who commits adultery lacks sense; he who does it destroys himself. Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru. Wochita zimenezi amangodziwononga yekha.
33 He will get wounds and dishonor, and his disgrace will not be wiped away. Adzalandira mabala ndi mʼnyozo, ndipo manyazi ake sadzamuchokera.
34 For jealousy makes a man furious, and he will show no mercy in the day of vengeance. Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa, ndipo sadzachita chifundo pobwezera.
35 He will accept no compensation; he will refuse no matter how large the bribe. Iye savomera dipo lililonse; sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]