Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 My son, pay attention to my wisdom; listen closely to my understanding, Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi, tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa,
2 so that you may guard discretion and your lips may preserve knowledge. kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo.
3 For the lips of the forbidden woman drip honey, and her mouth is smoother than oil, Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi. Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,
4 but in the end she is bitter as poison, sharp as a double-edged sword. koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu; ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.
5 Her feet go down to death; her steps take hold of the grave. Mapazi ake amatsikira ku imfa; akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.
6 She gives no thought to the path of life; her ways wander, and she does not know it. Iye saganizirapo za njira ya moyo; njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.
7 And now, my sons, listen to me, and do not turn away from the words of my mouth. Tsopano ana inu, mundimvere; musawasiye mawu anga.
8 Keep your way far from her, and do not go near the door of her house, Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo, usayandikire khomo la nyumba yake,
9 lest you give your honor to others and your years to one who is cruel, kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena; ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,
10 lest strangers take their fill of your strength, and your hard-earned labors go to the house of a foreigner, kapenanso alendo angadyerere chuma chako ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.
11 and at your end you groan, when your flesh and body are consumed, Potsiriza pa moyo wako udzabuwula, thupi lako lonse litatheratu.
12 and you say, "How I hated discipline, and my heart despised correction! Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo! Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!
13 I did not listen to the voice of my teachers or heed my instructors. Sindinamvere aphunzitsi anga kapena alangizi anga.
14 I was at the brink of utter ruin in the midst of the assembled congregation." Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke pakati pa msonkhano wonse.”
15 Drink water from your own cistern, flowing water from your own well. Imwa madzi a mʼchitsime chakochako, madzi abwino ochokera mʼchitsime chako.
16 Should your springs overflow in the streets, your streams of water in the public squares? Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu? Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda?
17 Let them be yours alone, and not shared with strangers. Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha, osati uyigawireko alendo.
18 May your fountain be blessed, and rejoice in the wife of your youth, Yehova adalitse kasupe wako, ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.
19 a loving doe, a graceful deer. May her love satisfy you always; may you be captivated continually by her love. Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino. Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse, ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
20 Why then, my son, should you be captivated by a forbidden woman and embrace another man's wife? Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo? Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?
21 For a man's ways are before the eyes of our Father, and he examines all the man's paths. Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona, ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.
22 The wicked are caught by their own wrongdoing and held fast in the cords of their sin. Ntchito zoyipa za munthu woyipa zimamukola yekha; zingwe za tchimo lake zimamumanga yekha.
23 He will die for lack of discipline, and he will go astray because of his great foolishness. Iye adzafa chifukwa chosowa mwambo, adzasocheretsedwa chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]