Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 4 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Listen, my children, to a father's instruction; pay attention, and gain understanding. Ananu, mverani malangizo a abambo anu; tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.
2 I am giving you sound teaching, so do not abandon my instruction. Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino. Choncho musasiye malangizo anga.
3 For I too was a son to my father, tender and the only beloved of my mother. Paja ndinalinso mwana mʼnyumba mwa abambo anga; mwana mmodzi yekha wapamtima pa amayi anga.
4 He taught me and said, "Let your heart hold on to my words; keep my commands and you will live. Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti, “Ugwiritse mawu anga pa mtima pako, usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.
5 Get wisdom, get understanding; do not forget, and do not turn away from the words of my mouth. Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu; usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.
6 Do not forsake her, and she will protect you; love her, and she will watch over you. Usasiye nzeru ndipo idzakusunga. Uziyikonda ndipo idzakuteteza.
7 The beginning of wisdom is this: get wisdom; and with all you acquire, get understanding. Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru. Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.
8 Cherish her, and she will lift you high; embrace her, and she will bring you honor. Uyilemekeze nzeruyo ndipo idzakukweza; ikumbatire nzeruyo ndipo idzakupatsa ulemu.
9 She will set a garland of grace on your head; she will present you with a crown of glory." Idzayika sangamutu yokongola yamaluwa pamutu pako; idzakupatsa chipewa chaufumu chaulemu.”
10 Listen, my son, and receive my words, and the years of your life will be many. Mwana wanga, umvere ndi kuvomereza zimene ndikunena, ndipo zaka za moyo wako zidzakhala zochuluka.
11 I have taught you the way of wisdom; I have led you along straight paths. Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera mʼnjira zolungama.
12 When you walk, your steps will not be held back; and when you run, you will not stumble. Pamene ukuyenda, mapazi ako sadzawombana; ukamadzathamanga, sudzapunthwa.
13 Hold on to instruction, do not let go; guard her, for she is your life. Ugwiritse zimene ndikukuphunzitsazi osazitaya ayi. Uwasamale bwino pakuti moyo wako wagona pamenepa.
14 Do not set foot on the path of the wicked, and do not walk in the way of evildoers. Usayende mʼnjira za anthu oyipa kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa.
15 Avoid it, do not travel on it; turn away from it and pass on by. Pewa njira zawo, usayende mʼmenemo; uzilambalala nʼkumangopita.
16 For they cannot sleep unless they do wrong; they are robbed of rest unless they make someone stumble. Pakuti iwo sagona mpaka atachita zoyipa; tulo salipeza mpaka atapunthwitsa munthu wina.
17 They feed on the bread of wickedness and drink the wine of violence. Paja chakudya chawo ndicho kuchita zoyipa basi ndipo chakumwa chawo ndi chiwawa.
18 But the path of the righteous is like the light of dawn, shining brighter and brighter until the full light of day. Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.
19 The way of the wicked is like deep darkness; they do not know what makes them stumble. Koma njira ya anthu oyipa ili ngati mdima wandiweyani; iwo sadziwa chomwe chimawapunthwitsa.
20 My son, pay attention to my words; listen closely to my sayings. Mwana wanga, mvetsetsa zimene ndikunena; tchera khutu ku mawu anga.
21 Never lose sight of them; keep them deep within your heart. Usayiwale malangizo angawa, koma uwasunge mu mtima mwako.
22 For they are life to those who find them, and healing to their whole body. Pakuti amapatsa moyo kwa aliyense amene awapeza ndipo amachiritsa thupi lake lonse.
23 Above all else, guard your heart, for everything you do flows from it. Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu pakuti ndiwo magwero a moyo.
24 Keep crooked speech from your mouth, and keep deceitful lips far from you. Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota; ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa.
25 Let your eyes look straight ahead; fix your gaze directly before you. Maso ako ayangʼane patsogolo; uziyangʼana kutsogolo molunjika.
26 Give careful thought to the path for your feet, and all your ways will be secure. Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa.
27 Do not turn to the right or the left; keep your foot away from evil. Usapatukire kumanja kapena kumanzere; usapite kumene kuli zoyipa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]