Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 My son, do not forget my teaching, but let your heart keep my commandments, Mwana wanga, usayiwale malangizo anga, mtima wako usunge malamulo anga.
2 for they will add length of days and years of life and peace to you. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka ndipo udzakhala pa mtendere.
3 Do not let covenant love and faithfulness leave you; bind them around your neck, write them on the tablet of your heart. Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako.
4 So you will find favor and a good reputation with our Father and with people. Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu.
5 Trust in our Father with all your heart, and do not lean on your own understanding. Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
6 In all your ways know him, and he will make your paths straight. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.
7 Do not be wise in your own eyes; fear our Father, and turn away from evil. Usamadzione ngati wa nzeru. Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa.
8 This will bring healing to your body and refreshment to your bones. Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino ndi mafupa ako adzakhala olimba.
9 Honor our Father with your wealth and with the firstfruits of all your produce, Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova.
10 then your barns will be filled with plenty, and your vats will overflow with new wine. Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.
11 My son, do not despise the discipline of our Father or be weary of his correction, Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova, ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.
12 for our Father disciplines the one his heart loves, just as a father disciplines the son he delights in. Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda, monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.
13 Blessed is the one who finds wisdom, and the one who gains understanding, Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,
14 for the gain from her is better than gain from silver, and her profit better than gold. pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva, phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide.
15 She is more precious than jewels, and nothing you desire can compare with her. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali; ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru.
16 Long life is in her right hand; in her left hand are riches and honor. Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali; mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu.
17 Her ways are pleasant, and all her paths are peace. Njira zake ndi njira zosangalatsa, ndipo mu njira zake zonse muli mtendere.
18 She is a tree of life to those who take hold of her; those who hold her fast are called blessed. Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa; wodala munthu amene amayigwiritsa kwambiri.
19 Our Father by wisdom founded the earth; by understanding he established the heavens; Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru. Anagwiritsanso ntchito nzeru zakudziwa bwino zinthu pamene ankakhazikitsa zakumwamba.
20 by his knowledge the depths burst open, and the clouds drop down the dew. Mwa nzeru zake Yehova anatumphutsa madzi kuchokera mʼnthaka ndiponso mitambo inagwetsa mvula.
21 My son, do not lose sight of these; keep sound wisdom and discretion, Mwana wanga usunge nzeru yeniyeni ndi khalidwe lomalingarira zinthu bwino. Zimenezi zisakuchokere.
22 and they will be life for your soul and an adornment for your neck. Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wosangalatsa ndi wabwino ngati mkanda wa mʼkhosi.
23 Then you will walk on your way securely, and your foot will not stumble. Choncho udzayenda pa njira yako mosaopa kanthu, ndipo phazi lako silidzapunthwa;
24 If you lie down, you will not be afraid; when you lie down, your sleep will be sweet. pamene ugona pansi, sudzachita mantha; ukadzagona pansi tulo tako tidzakhala tokoma.
25 Do not be afraid of sudden terror, or of the ruin of the wicked when it comes, Usaope tsoka lobwera mwadzidzidzi kapena chiwonongeko chimene chidzagwera anthu oyipa,
26 for our Father will be your confidence and will keep your foot from being caught. pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima ndipo adzasunga phazi lako kuti lisakodwe mu msampha.
27 Do not withhold good from those who deserve it, when it is in your power to do it. Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino, pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi.
28 Do not say to your neighbor, "Go, and come back, and tomorrow I will give it"—when you have it with you. Usanene kwa mnansi wako kuti, “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa” pamene uli nazo tsopano.
29 Do not plot evil against your neighbor, who lives trustingly beside you. Usamukonzere chiwembu mnansi wako, amene anakhala nawe pafupi mokudalira.
30 Do not quarrel with anyone for no reason, when he has done you no harm. Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa pamene iye sanakuchitire zoyipa.
31 Do not envy a violent man, and do not choose any of his ways, Usachite naye nsanje munthu wachiwawa kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse.
32 for the devious person is detestable to our Father, but he takes the upright into his confidence. Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa koma amayanjana nawo anthu olungama.
33 The curse of our Father is on the house of the wicked, but he blesses the home of the righteous. Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa, koma amadalitsa nyumba ya anthu olungama.
34 Toward the mockers he is scornful, but to the humble he gives grace. Anthu onyoza, Iye amawanyoza, koma amakomera mtima anthu odzichepetsa.
35 The wise will inherit honor, but fools get only disgrace. Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]