Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 My son, if you receive my words and store up my commandments within you, Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,
2 making your ear attentive to wisdom and turning your heart toward understanding; ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;
3 yes, if you call out for insight and raise your voice for understanding, ngati upempha kuti uzindikire zinthu inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,
4 if you seek it like silver and search for it as for hidden treasure, ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,
5 then you will understand the fear of our Father and find the knowledge of our Father. ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.
6 For our Father gives wisdom; from his mouth come knowledge and understanding. Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.
7 He stores up sound wisdom for the upright; he is a shield to those who walk in integrity, Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo. Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
8 guarding the paths of justice and watching over the way of his faithful ones. pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama. Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.
9 Then you will understand righteousness and justice and fairness—every good path. Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo, kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.
10 For wisdom will enter your heart, and knowledge will be pleasant to your soul; Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako, kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.
11 discretion will watch over you, and understanding will guard you, Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga; kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.
12 rescuing you from the way of evil, from men who speak twisted things, Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa, kwa anthu amabodza,
13 who abandon the paths of uprightness to walk in the ways of darkness, amene amasiya njira zolungama namayenda mʼnjira zamdima,
14 who delight in doing evil and rejoice in the perversity of evil, amene amakondwera pochita zoyipa namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.
15 whose paths are crooked, and who are devious in their ways. Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota, ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.
16 Wisdom will rescue you also from the forbidden woman, from the stranger with her smooth words, Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo; kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika,
17 who forsakes the companion of her youth and forgets the covenant of her Father. amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.
18 For her house sinks down to death, and her paths to the dead. Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa; njira zake zimamufikitsa ku manda.
19 None who go to her return, nor do they reach the paths of life. Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera kapena kupezanso njira zamoyo.
20 So you will walk in the way of the good and keep to the paths of the righteous. Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino, uzitsata njira za anthu ochita chilungamo.
21 For the upright will live in the land, and those of integrity will remain in it; Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo;
22 but the wicked will be cut off from the land, and the treacherous will be torn away from it. Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo, ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]