Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The proverbs of Solomon, son of David, king of Israel: Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:
2 To know wisdom and instruction, to understand words of insight, Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo; kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;
3 to receive instruction in wise conduct, in righteousness, justice, and fairness, kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru, akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.
4 to give prudence to the simple, knowledge and discretion to the young, Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera, achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.
5 let the wise also hear and increase in learning, and let the one who understands gain guidance, Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake, ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,
6 to understand a proverb and a parable, the words of the wise and their riddles. kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo, mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.
7 The fear of our Father is the beginning of knowledge; fools despise wisdom and instruction. Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
8 Listen, my son, to your father's instruction, and don't turn away from your mother's teaching, Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
9 for they are a graceful garland for your head and pendants for your neck. Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.
10 My son, if sinners entice you, do not give in. Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa usamawamvere.
11 If they say, "Come with us, let us lie in wait for blood, let us ambush the innocent without cause; Akadzati, “Tiye kuno; tikabisale kuti tiphe anthu, tikabisalire anthu osalakwa;
12 like the grave let us swallow them alive, and whole, like those who go down to the pit; tiwameze amoyo ngati manda, ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje.
13 we will find all kinds of precious goods, we will fill our houses with plunder; Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda;
14 throw in your lot with us; we will all share one purse," Bwera, chita nafe maere, ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.”
15 my son, do not walk in the way with them; hold back your foot from their paths, Mwana wanga, usayende nawo pamodzi, usatsagane nawo mʼnjira zawozo.
16 for their feet run to evil, and they hurry to shed blood. Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha, amathamangira kukhetsa magazi.
17 For a net spread out before any bird's eyes catches nothing; Nʼkopanda phindu kutchera msampha mbalame zikuona!
18 but these lie in wait for their own blood; they ambush their own lives. Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe; amangodzitchera okha msampha!
19 Such are the ways of everyone greedy for unjust gain; it takes away the life of its possessors. Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza; chumacho chimapha mwiniwake.
20 Wisdom cries aloud in the street; in the open squares she lifts her voice. Nzeru ikufuwula mu msewu, ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika;
21 At the head of the noisy streets she calls out; at the entrance of the city gates she speaks: ikufuwula pa mphambano ya misewu, ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti,
22 "How long, simple ones, will you love being simple? How long will mockers delight in their mocking and fools hate knowledge? “Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti? Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti? Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?
23 If you respond to my correction, I, Wisdom, will pour out my spirit on you; I will make my words known to you. Tamverani mawu anga a chidzudzulo. Ine ndikukuwuzani maganizo anga ndi kukudziwitsani mawu anga.
24 Because I have called and you refused, I stretched out my hand and no one paid attention, Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera. Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala.
25 and you ignored all my counsel and rejected all my correction, Uphungu wanga munawunyoza. Kudzudzula kwanga simunakusamale.
26 I also will laugh at your calamity; I will mock when terror overtakes you, Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto; ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.
27 when terror overtakes you like a storm and your calamity comes like a whirlwind, when distress and anguish come upon you. Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe, tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu, mavuto ndi masautso akadzakugwerani.
28 Then they will call on me, but I will not answer; they will seek me earnestly but will not find me, “Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha; mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.
29 because they hated knowledge and did not choose the fear of our Father, Popeza iwo anadana ndi chidziwitso ndipo sanasankhe kuopa Yehova,
30 they rejected my counsel and despised all my correction. popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa.
31 So they will eat the fruit of their own way and have their fill of their own schemes. Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.
32 For the waywardness of the simple will kill them, and the complacency of fools will destroy them; Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo, ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo.
33 but whoever listens to me will dwell secure and be at ease, without dread of disaster." Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata; adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]