Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 35 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The wilderness and the dry land will be glad; the desert will rejoice and blossom like the crocus. Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala; dziko lowuma lidzakondwa ndi kuchita maluwa.
2 It will blossom abundantly and rejoice with joy and singing. The glory of Lebanon will be given to it, the splendor of Carmel and Sharon. They will see the glory of our Father, the majesty of our Father. Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu.
3 Strengthen the weak hands, and steady the buckling knees. Limbitsani manja ofowoka, limbitsani mawondo agwedegwede;
4 Say to those with an anxious heart, "Be strong; do not fear! Look, your Father will come with justice, with our Father's retribution. He will come and save you." nenani kwa a mitima yamantha kuti; “Limbani mtima, musachite mantha; Mulungu wanu akubwera, akubwera kudzalipsira; ndi kudzabwezera chilango adani anu; akubwera kudzakupulumutsani.”
5 Then the eyes of the blind will be opened, and the ears of the deaf unstopped. Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
6 Then the lame will leap like a deer, and the tongue of the mute will sing for joy. For waters will break forth in the wilderness, and streams in the desert. Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala, ndipo osayankhula adzayimba mokondwera. Akasupe adzatumphuka mʼchipululu ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
7 The burning sand will become a pool, and the thirsty ground springs of water; in the haunt where jackals lie down, the grass will become reeds and rushes. mchenga wotentha udzasanduka dziwe, nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe. Pamene panali mbuto ya ankhandwe padzamera udzu ndi bango.
8 And a highway will be there, a road, and it will be called the Way of Holiness. The unclean will not travel it; it belongs to the one who walks the way—even fools will not go astray. Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu; ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika. Anthu odetsedwa sadzayendamo mʼmenemo; zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
9 No lion will be there, nor will any ravenous beast travel on it; they will not be found there. But the redeemed will walk there, Kumeneko sikudzakhala mkango, ngakhale nyama yolusa sidzafikako; sidzapezeka konse kumeneko. Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.
10 and the ransomed of our Father will return. They will come to Zion with singing, everlasting joy upon their heads; gladness and joy will overtake them, and sorrow and sighing will flee away. Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera. Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba; kumeneko adzakondwa mpaka muyaya. Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe, ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]