Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The word that Isaiah son of Amoz saw concerning Judah and Jerusalem. Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:
2 In the last days the mountain of our Father's house will be firmly established as the highest of the mountains, raised above the hills, and all the nations will stream to it. Mʼmasiku otsiriza, phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse, lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse, ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.
3 Many peoples will come and say, "Come, let us go up to the mountain of God, to his house, so he can teach us his ways and we can walk in his paths." For instruction will go out from Zion, and the word of our Father from Jerusalem. Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.” Malangizo adzachokera ku Ziyoni, mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
4 He will judge between the nations and settle disputes for many peoples. They will beat their swords into plowshares and their spears into pruning hooks; nation will not lift up sword against nation, nor will they train for war anymore. Iye adzaweruza pakati pa mayiko, ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri. Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera. Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina, kapena kuphunziranso za nkhondo.
5 House of Jacob, come, let us walk in the light of our Father. Inu nyumba ya Yakobo, bwerani, tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.
6 For you have abandoned your people, the house of Jacob, because they are filled with influences from the east and with fortune-tellers like the Philistines, and they have made alliances with foreigners. Inu Yehova mwawakana anthu anu, nyumba ya Yakobo. Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa; amawombeza mawula ngati Afilisti, ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.
7 Their land is full of silver and gold, with no end to their treasures; their land is full of horses, with no end to their chariots. Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide; ndipo chuma chawo ndi chosatha. Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo; ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka.
8 Their land is full of idols; they bow down to the work of their hands, to what their own fingers have made. Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano; iwo amapembedza ntchito ya manja awo, amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.
9 So mankind is brought low, and everyone is humbled—do not forgive them. Tsono munthu aliyense adzachepetsedwa ndi kutsitsidwa. Inu Yehova musawakhululukire.
10 Go into the rocks and hide in the dust from the dread of our Father and from the splendor of his majesty. Lowani mʼmatanthwe, bisalani mʼmaenje, kuthawa kuopsa kwa Yehova ndi ulemerero wa ufumu wake!
11 The proud eyes of mankind will be brought low, and the arrogance of men will be humbled; our Father alone will be exalted in that day. Kudzikuza kwa anthu kudzatha, ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa; Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.
12 For the Father of heaven's armies has a day in store against all that is proud and lofty, against all that is lifted up, so that it will be brought low, Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu,
13 against all the cedars of Lebanon, lofty and lifted up, and against all the oaks of Bashan, tsiku la mikungudza yonse ya ku Lebanoni, yayitali ndi yoonekera patali, ndiponso la mitengo yonse ya thundu ya ku Basani,
14 against all the high mountains and against all the lofty hills, tsiku la mapiri onse ataliatali ndiponso la zitunda zonse zazitali,
15 against every high tower and against every fortified wall, tsiku la nsanja zonse zazitali ndiponso malinga onse olimba,
16 against all the ships of Tarshish and against every magnificent vessel. tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi ndiponso la mabwato onse okongola.
17 The arrogance of mankind will be humbled, and the pride of men brought low; our Father alone will be exalted in that day, Kudzikuza kwa munthu kudzatha ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa, Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo,
18 and the idols will completely vanish. ndipo mafano onse adzatheratu.
19 People will flee into the caves of the rocks and into holes in the ground from the dread of our Father and from the splendor of his majesty, when he rises to shake the earth. Anthu adzathawira mʼmapanga a matanthwe ndi mʼmaenje a nthaka, kuthawa mkwiyo wa Yehova, ndiponso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
20 In that day people will throw away their idols of silver and their idols of gold to the moles and bats, which they made for themselves to worship. Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide, amene anawapanga kuti aziwapembedza.
21 They will go into the clefts of the rocks and into the crevices of the cliffs from the dread of our Father and from the splendor of his majesty, when he rises to shake the earth. Adzathawira mʼmapanga a matanthwe ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka kuthawa mkwiyo wa Yehova ndiponso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
22 Stop trusting in mere man, who has only breath in his nostrils. What good is he? Lekani kudalira munthu, amene moyo wake sukhalira kutha. Iye angathandize bwanji wina aliyense?
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]