Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The vision of Isaiah son of Amoz concerning Judah and Jerusalem in the days of Uzziah, Jotham, Ahaz, and Hezekiah, kings of Judah. Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.
2 Hear, heavens, and listen, earth, for our Heavenly Father has spoken: "Children I reared and brought up, but they have rebelled against me. Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi! Pakuti Yehova wanena kuti, “Ndinabala ana ndi kuwalera, koma anawo andiwukira Ine.
3 "The ox knows its owner, and the donkey its master's manger, but Israel does not know, my people do not understand. Ngʼombe imadziwa mwini wake, bulu amadziwa kumene kuli gome la mbuye wake, koma Israeli sadziwa, anthu anga samvetsa konse.”
4 Ah, sinful nation, a people weighed down with guilt, offspring of evildoers, children who act corruptly! They have forsaken our Father, they have spurned the Holy One of Israel—our Father—they have turned their backs and walked away. Haa, mtundu wochimwa, anthu olemedwa ndi machimo, obadwa kwa anthu ochita zoyipa, ana odzipereka ku zoyipa! Iwo asiya Yehova; anyoza Woyerayo wa Israeli ndipo afulatira Iyeyo.
5 Why will you be beaten any longer? Why do you keep on rebelling? The whole head is sick, and the whole heart is faint. Chifukwa chiyani mukufuna kuti muzingolangidwabe? Chifukwa chiyani mukupitirira kukhala mʼmoyo wowukira? Mutu wanu wonse uli ndi mabala, mtima wanu wonse wafowokeratu.
6 From the sole of the foot to the top of the head there is no healthy spot—only wounds, welts, and open sores, not cleaned or bandaged or soothed with oil. Kuchokera ku phazi mpaka ku mutu palibe pabwino, paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda, mabala ali magazi chuchuchu, mabala ake ngosatsuka, ngosamanga ndiponso ngosapaka mafuta ofewetsa.
7 Your land is desolate, your cities burned with fire; in your very presence foreigners devour your fields—a desolation, overthrown by strangers. Dziko lanu lasanduka bwinja, mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; minda yanu ikukololedwa ndi alendo inu muli pomwepo, dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.
8 And the daughter of Zion is left like a shelter in a vineyard, like a hut in a cucumber field, like a city under siege. Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha ngati nsanja mʼmunda wampesa, ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
9 If the Father of heaven's armies had not left us a few survivors, we would have become like Sodom, we would have been like Gomorrah. Yehova Wamphamvuzonse akanapanda kutisiyira opulumuka, tikanawonongeka ngati Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.
10 Hear the word of our Father, you rulers of Sodom! Listen to the instruction of our Father, you people of Gomorrah! Imvani mawu a Yehova, inu olamulira Sodomu; mverani lamulo la Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora!
11 What are your endless sacrifices to me?" says our Father. "I have had my fill of burnt offerings of rams and the fat of fattened animals; I take no delight in the blood of bulls and lambs and goats. Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani nsembe zanu zochuluka?” “Zandikola nsembe zanu zopsereza za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa; sindikusangalatsidwanso ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.
12 When you come to appear before me, who asked this of you—this trampling of my courts? Ndani anakulamulirani kuti mubwere nazo pamaso panga? Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?
13 Stop bringing meaningless offerings! Your incense is detestable to me. New moons, Sabbaths, the calling of assemblies—I cannot stand wickedness mixed with your solemn gatherings. Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo! Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine. Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa, kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.
14 Your new moons and your appointed feasts my soul hates; they have become a burden to me—I am weary of carrying them. Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera; ndatopa kuzinyamula.
15 When you stretch out your hands in prayer, I will hide my eyes from you; even when you offer many prayers, I will not be listening. Your hands are full of blood. Mukamatambasula manja anu popemphera, Ine sindidzakuyangʼanani; ngakhale muchulukitse mapemphero anu, sindidzakumverani. Manja anu ndi odzaza ndi magazi;
16 Wash yourselves; make yourselves clean. Take your evil deeds out of my sight; stop doing wrong. sambani, dziyeretseni. Chotsani pamaso panu ntchito zanu zoyipa! Lekani kuchita zoyipa,
17 Learn to do good; seek justice, set the oppressor right. Defend the orphan, stand up for the widow. phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
18 Come now, let us settle this together," says our Father. "Though your sins are like scarlet, they will be as white as snow; though they are red as crimson, they will become like wool. Yehova akuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu. Ngakhale machimo anu ali ofiira, adzayera ngati thonje. Ngakhale ali ofiira ngati kapezi, adzayera ngati ubweya wankhosa.
19 If you are willing and obedient, you will eat the good things of the land; Ngati muli okonzeka kundimvera mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
20 but if you refuse and rebel, you will be devoured by the sword. For the mouth of our Father has spoken." koma mukakana ndi kuwukira mudzaphedwa ndi lupanga.” Pakuti Yehova wayankhula.
21 How the faithful city has become a prostitute! She was once full of justice; righteousness used to dwell in her—but now murderers. Taonani momwe mzinda wokhulupirika wasandukira wadama! Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama; mu mzindamo munali chilungamo, koma tsopano muli anthu opha anzawo!
22 Your silver has become worthless slag, your choice wine diluted with water. Siliva wako wasanduka wachabechabe, vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi.
23 Your rulers are rebels, partners with thieves; they all love a bribe and chase after gifts. They do not defend the orphan, and the widow gets no hearing from them. Atsogoleri ako ndi owukira, anthu ogwirizana ndi mbala; onse amakonda ziphuphu ndipo amathamangira mphatso. Iwo sateteza ana amasiye; ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.
24 Therefore this is the declaration of the Sovereign Father, the Father of heaven's armies, the Mighty One of Israel—our Father: Ah, I will get relief from my adversaries and bring justice against my foes. Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu, Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti, “Haa, odana nane ndidzawatha, ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.
25 I will turn my hand against you; I will smelt away your slag as with lye and remove all your impurities. Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe; ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa, monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
26 I will restore your judges as in days of old, your counselors as at the beginning. Afterward you will be called the City of Righteousness, the Faithful City. Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana, aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja. Kenaka iweyo udzatchedwa mzinda wolungama, mzinda wokhulupirika.”
27 Zion will be redeemed by justice, and those in her who repent, by righteousness. Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama, anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo.
28 But rebels and sinners will be broken together, and those who forsake our Father will be consumed. Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi, ndipo amene asiya Yehova adzatheratu.
29 You will be ashamed of the sacred oaks you delighted in; you will blush over the gardens you have chosen. “Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu imene inkakusangalatsani; mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda imene munayipatula.
30 For you will be like an oak whose leaves wither, like a garden without water. Mudzakhala ngati mtengo wa thundu umene masamba ake akufota, mudzakhala ngati munda wopanda madzi.
31 The strong man will become tinder and his work a spark; both will burn together, with no one to put them out. Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma, ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali; motero zonse zidzayakira limodzi, popanda woti azimitse motowo.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]