Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 For look—the Father of heaven's armies is about to strip from Jerusalem and from Judah every support and supply: the whole supply of bread and the whole supply of water, Taonani tsopano, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda zinthu pamodzi ndi thandizo; adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
2 the warrior and the soldier, the judge and the prophet, the fortune-teller and the elder, anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo, oweruza ndi aneneri, anthu olosera ndi akuluakulu,
3 the commander of fifty and the man of rank, the counselor, the skilled craftsman, and the clever enchanter. atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka, aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
4 "I will make mere boys their officials, and childish whim will rule over them. Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo; ana akhanda ndiwo adzawalamulire.
5 The people will oppress one another, each man against his neighbor; the young will rise up against the old, and the lowly against the honored." Anthu adzazunzana, munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake. Anthu wamba adzanyoza akuluakulu.
6 A man will seize his brother in his father's house and say, "You have a coat—you be our leader; take charge of this heap of ruins." Munthu adzagwira mʼbale wake mʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati, “Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu; lamulira malo opasuka ano!”
7 But on that day he will cry out, "I am no healer! There is no bread and no coat in my house—you will not make me leader of the people." Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti, “Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake. Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga; musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
8 For Jerusalem has stumbled and Judah has fallen, because their words and their deeds are against our Father, defying his glorious presence. Yerusalemu akudzandira, Yuda akugwa; zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova, sakulabadira ulemerero wa Mulungu.
9 The look on their faces testifies against them; they flaunt their sin like Sodom—they do not hide it. How terrible for them, for they have brought disaster on themselves! Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa; amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu; salibisa tchimo lawolo. Tsoka kwa iwo odziputira okha mavuto.
10 Tell the righteous it will go well with them, for they will eat the fruit of their deeds. Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino, pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.
11 How terrible for the wicked! It will go badly for him, for what his hands have done will be repaid to him. Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo! Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.
12 My people—children are their oppressors, and women rule over them. My people, your guides lead you astray and have swallowed up the path you should walk. Achinyamata akupondereza anthu anga, ndipo amene akuwalamulira ndi akazi. Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani; akukuchotsani pa njira yanu.
13 Our Father takes his stand to bring his case; he rises to judge the peoples. Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu; wakonzeka kuti aweruze anthu ake.
14 Our Father enters into judgment with the elders and officials of his people: "It is you who have devoured the vineyard; the plunder of the poor is in your houses. Yehova akuwazenga milandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake: “Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa; nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
15 What do you mean by crushing my people and grinding the faces of the poor?" declares the Father of heaven's armies. Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga, nʼkudyera masuku pamutu amphawi?” Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
16 Our Father said: "Because the daughters of Zion are proud—walking with outstretched necks and flirting eyes, mincing along with quick little steps, jingling the anklets on their feet, Yehova akunena kuti, “Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri, akuyenda atakweza makosi awo, akukopa amuna ndi maso awo akuyenda monyangʼama akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
17 therefore the Sovereign Father will strike the heads of the daughters of Zion with scabs, and our Father will lay bare their foreheads." Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo; Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”
18 On that day the Sovereign Father will strip away their finery: the anklets, the headbands, the crescent ornaments, Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi,
19 the earrings, the bracelets, the veils, ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope,
20 the headdresses, the ankle chains, the sashes, the perfume flasks, the charms, maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa,
21 the signet rings, the nose rings, mphete ndi zipini,
22 the festival robes, the capes, the cloaks, the purses, zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama,
23 the hand mirrors, the fine linen garments, the turbans, and the shawls. magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.
24 Then, instead of perfume there will be a stench; instead of a sash, a rope; instead of elegantly styled hair, baldness; instead of fine robes, a wrapping of coarse cloth; branding instead of beauty. Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha, mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe; mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi; mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli; mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
25 Your men will fall by the sword, your warriors in the battle. Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga, asilikali ako adzafera ku nkhondo.
26 Her gates will mourn and lament; stripped bare, she will sit on the ground. Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira; Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]