Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 4 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 On that day seven women will take hold of one man, saying, "We will eat our own bread and wear our own clothes; only let us be called by your name. Take away our disgrace." Tsiku limenelo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi, nʼkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu, ndi kuvala zovala zathu; inu mungotilola kuti tidziyitanidwa ndi dzina lanu. Tichotseni manyazi aumbeta!”
2 On that day the Branch of our Father will be beautiful and glorious, and the fruit of the land will be the pride and splendor of the survivors of Israel. Tsiku limenelo Nthambi ya Yehova idzakhala yokongola ndi yaulemerero, ndipo chipatso cha mʼdziko chidzakhala chonyaditsa ndi chopereka ulemerero kwa onse opulumuka mu Israeli.
3 And whoever is left in Zion and remains in Jerusalem will be called holy—everyone recorded for life in Jerusalem, Iwo amene adzatsale mu Ziyoni, amene adzatsalire mu Yerusalemu, adzatchedwa oyera, onse amene mayina awo alembedwa pakati pa anthu amoyo okhala mu Yerusalemu.
4 when the Sovereign Father has washed away the filth of the daughters of Zion and rinsed the bloodstains of Jerusalem from within her by a spirit of judgment and a spirit of burning. Ambuye adzasambitsa akazi a Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zawo. Adzatsuka magazi amene anakhetsedwa mu Yerusalemu ndi mzimu wachiweruzo ndiponso mzimu wamoto.
5 Then our Father will create over the whole site of Mount Zion and over her assemblies a cloud by day and smoke, and a bright, flaming fire by night; for there will be a canopy over all the glory. Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova.
6 It will be a shelter to give shade from the heat by day, and a refuge and hiding place from storm and rain. Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothawiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi owusiramo mvula.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]