Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Let me sing now for the one I love a song of my beloved about his vineyard. My beloved had a vineyard on a very fertile hillside. Ndidzamuyimbira bwenzi langa nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa: Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa pa phiri la nthaka yachonde.
2 He dug it and cleared it of stones and planted it with the choicest vines. He built a watchtower in the middle of it and also carved out a winepress in it. Then he waited for it to yield good grapes, but it yielded only wild ones. Anatipula nachotsa miyala yonse ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri. Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo. Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ayi, unabala mphesa zosadya.
3 "And now, you who live in Jerusalem and you people of Judah, judge between me and my vineyard. “Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda, weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
4 What more was there to do for my vineyard that I have not done in it? Why, when I waited for it to yield good grapes, did it yield only wild ones? Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa kupambana chomwe ndawuchitira kale? Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino, bwanji unabala mphesa zosadya?
5 And now let me tell you what I am about to do to my vineyard: I will take away its hedge, and it will be devoured; I will break down its wall, and it will be trampled. Tsopano ndikuwuzani chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa: ndidzachotsa mpanda wake, ndipo mundawo udzawonongeka; ndidzagwetsa khoma lake, ndipo nyama zidzapondapondamo.
6 I will make it a wasteland; it will not be pruned or hoed, and briers and thorns will grow up over it. And I will command the clouds to send no rain upon it." Ndidzawusandutsa tsala, udzakhala wosatengulira ndi wosalimira ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina. Ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pa mundapo.”
7 For the vineyard of the Father of heaven's armies is the house of Israel, and the people of Judah are his cherished planting. He looked for justice, but found only bloodshed; for righteousness, but heard only an outcry. Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse ndi Aisraeli, ndipo anthu a ku Yuda ndiwo minda yake yomukondweretsa. Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana; mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.
8 Woe to those who add house to house and join field to field, until there is no room left and you live alone in the middle of the land. Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba, ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda, mpaka mutalanda malo onse kuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo.
9 With my own ears I heard the Father of heaven's armies swear: "Surely many houses will become desolate, great and beautiful ones left without anyone to live in them. Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti, “Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja, nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
10 For ten acres of vineyard will yield only about six gallons of wine, and ten baskets of seed will yield only one basket of grain." Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi, kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”
11 Woe to those who rise early in the morning to chase strong drink, who linger late into the evening till wine inflames them. Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawa nathamangira chakumwa choledzeretsa, amene amamwa mpaka usiku kufikira ataledzera kotheratu.
12 At their feasts there are lyre and harp, tambourine and flute and wine, but they pay no regard to the deeds of our Father, and they do not see the work of his hands. Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe, matambolini, zitoliro ndi vinyo, ndipo sasamala ntchito za Yehova, salemekeza ntchito za manja ake.
13 Therefore my people go into exile for lack of knowledge; their honored men are starved, and the common people are parched with thirst. Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo chifukwa cha kusamvetsa zinthu; atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala, ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
14 Therefore the grave has enlarged its appetite and opened its mouth wide, and down go her splendor and her crowds, her uproar and all who rejoice in her. Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta ndipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake; mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka; adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko.
15 So mankind is humbled, and each person is brought low, and the proud eyes of the arrogant are cast down. Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa, anthu onse adzachepetsedwa, anthu odzikuza adzachita manyazi.
16 But the Father of heaven's armies is exalted in justice, and our holy Father shows himself holy in righteousness. Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama. Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.
17 Then lambs will graze as in their own pasture, and strangers will feed among the ruins of the rich. Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo; ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera.
18 Woe to those who drag their wickedness along with cords of lies, and sin as with cart ropes, Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo, ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo,
19 who say, "Let him hurry; let him speed his work, so we may see it. Let the plan of the Holy One of Israel draw near and come, so we may know it." amene amanena kuti, “Yehova afulumire, agwire ntchito yake mwamsanga kuti ntchitoyo tiyione. Ntchito zionekere, zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita, zichitike kuti tizione.”
20 Woe to those who call evil good and good evil, who call darkness light and light darkness, who call bitter sweet and sweet bitter. Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoyipa, amene mdima amawuyesa kuwala ndipo kuwala amakuyesa mdima, amene zowawasa amaziyesa zotsekemera ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.
21 Woe to those who are wise in their own eyes and clever in their own sight. Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru ndipo amadziyesa ochenjera.
22 Woe to those who are heroes at drinking wine and champions at mixing strong drink, Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo ndipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,
23 who acquit the guilty for a bribe and strip away the rights of the innocent. amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
24 Therefore, as a tongue of fire devours the stubble and dry grass shrivels in the flame, so their roots will rot and their blossom go up like dust; for they have rejected the instruction of the Father of heaven's armies, and despised the word of the Holy One of Israel. Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto, momwemonso mizu yawo idzawola ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi; chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse, ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
25 Therefore the anger of our Father burned against his people, and he stretched out his hand against them and struck them. The mountains quaked, and their corpses lay like garbage in the streets. For all this his anger has not turned away, and his hand is still stretched out. Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake; watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha Mapiri akugwedezeka, ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala. Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke, dzanja lake likanali chitambasulire;
26 He will raise a signal for the nations far away and whistle for them from the ends of the earth, and swiftly, speedily they come. Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali, akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi. Awo akubwera, akubweradi mofulumira kwambiri!
27 Not one of them is weary or stumbles, not one drowses or sleeps; not a belt is loosened at the waist, not a sandal strap is broken. Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa, palibe amene akusinza kapena kugona; palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka, palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka.
28 Their arrows are sharpened and all their bows are drawn; their horses' hooves seem like flint and their wheels like a whirlwind. Mivi yawo ndi yakuthwa, mauta awo onse ndi okoka, ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi, magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.
29 Their roar is like a lion; they roar like young lions. They growl and seize the prey and carry it off, with no one to rescue the victims. Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango, amabangula ngati misona ya mkango; imadzuma pamene ikugwira nyama ndipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.
30 On that day they will growl over it like the growling of the sea. And if anyone looks across the land, there is only darkness and distress; even the light is darkened by its clouds. Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula ngati mkokomo wa madzi a mʼnyanja. Ndipo wina akakayangʼana dzikolo adzangoona mdima ndi zovuta; ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]