Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 18 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Ah, land of whirring wings, beyond the rivers of Cush, Tsoka kwa anthu a ku Kusi. Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko a dzombe.
2 who sends ambassadors by the sea, in vessels of papyrus across the waters. Go, swift messengers, to a nation tall and smooth-skinned, to a people feared near and far, a nation mighty and trampling down, whose land the rivers divide. Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo, mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi, ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro, kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala, ndi woopedwa ndi anthu. Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena. Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”
3 All you inhabitants of the world, you who dwell on the earth: when a banner is raised on the mountains, look! When a trumpet sounds, listen! Inu nonse anthu a pa dziko lonse, inu amene mumakhala pa dziko lapansi, pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri yangʼanani, ndipo pamene lipenga lilira mumvere.
4 For this is what our Father said to me: I will be still, and I will look on from my dwelling place, like clear heat in the sunlight, like a cloud of dew in the heat of harvest. Pakuti Yehova akunena kwa ine kuti, “Ndili chikhalire ku malo anga kuno, ndidzakhala chete, ndi kumangoyangʼana, monga momwe dzuwa limawalira nthawi yotentha, monganso momwe mame amagwera usiku pa nthawi yotentha yokolola.”
5 For before the harvest, when the blossom is over and the bud becomes a ripening grape, our Father will cut off the shoots with pruning knives, and the spreading branches he will take away and lop off. Pakuti, anthu asanayambe kukolola, maluwa atayoyoka ndiponso mphesa zitayamba kupsa, Iye adzadula mphukira ndi mipeni yosadzira, ndipo adzadula ndi kuchotsa nthambi zotambalala.
6 They will all be left for the birds of prey of the mountains and for the beasts of the earth. The birds of prey will summer on them, and all the beasts of the earth will winter on them. Mitembo ya anthu ankhondo adzasiyira mbalame zamʼmapiri zodya nyama ndiponso zirombo zakuthengo; mbalame zidzadya mitemboyo nthawi yonse ya chilimwe, ndipo zirombo zidzayidya pa nthawi yonse yachisanu.
7 At that time gifts will be brought to the Father of heaven's armies, from a people tall and smooth-skinned, from a people feared near and far, a nation mighty and trampling down, whose land the rivers divide—to the place of the name of the Father of heaven's armies, Mount Zion. Pa nthawi imeneyo anthu adzabwera ndi mphatso kwa Yehova Wamphamvuzonse, zochokera kwa anthu ataliatali ndi osalala, kuchokera kwa mtundu wa anthu woopedwa ndi anthu apafupi ndi akutali omwe, mtundu wa anthu amphamvu ndi a chiyankhulo chachilendo, anthu amene dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje. Adzabwera nazo mphatso ku Phiri la Ziyoni, ku malo a Dzina la Yehova Wamphamvuzonse.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]