Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 17 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 An oracle about Damascus. Look—Damascus will no longer be a city; it becomes a heap of ruins. Uthenga wonena za Damasiko: “Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda, koma udzasanduka bwinja.
2 The cities of Aroer are abandoned; they will be left for the flocks, which will lie down with no one to frighten them. Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthu ndipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansi popanda wina woziopseza.
3 The fortress will vanish from Ephraim, and the kingdom from Damascus; and the remnant of Aram will be like the glory of the children of Israel, declares the Father of heaven's armies. Ku Efereimu sikudzakhalanso linga, ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu; Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu monga anthu a ku Israeli,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
4 In that day the glory of Jacob will be brought low, and the fat of his body will waste away. “Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira; ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi.
5 It will be as when a harvester gathers the standing grain and harvests the heads of grain with his arm; it will be as when someone gleans the grain in the Valley of Rephaim. Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu umene anatsiriza kukolola. Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
6 Yet a few will be left, as when an olive tree is beaten: two or three ripe olives at the very top, four or five on the fruitful branches, declares the Father of Israel. Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,” akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
7 In that day people will look to their Maker, and their eyes will turn to the Holy One of Israel—our Father. Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawo ndipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli.
8 They will not look to the altars, the work of their hands, and they will not gaze at what their own fingers have made—the Asherah poles and the incense altars. Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe, ntchito ya manja awo, ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera, ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
9 In that day their strong cities will be like the abandoned places of the woods and hilltops, which were deserted when the children of Israel came; and it will be a desolation. Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.
10 For you have forgotten the Father of your salvation, and you have not remembered the Rock of your refuge. Therefore, though you plant pleasant gardens and set out cuttings from a foreign vine, Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu; simunakumbukire Thanthwe, linga lanu. Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino, ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa,
11 and though on the day you plant them they begin to sprout, and by morning your planting is in blossom, yet the harvest will vanish in a day of grief and incurable pain. nimuyembekeza kuti zikule tsiku lomwelo ndi kuphukira maluwa mmawa mwake, komabe zimenezi sizidzakupindulirani pa tsiku la mavuto.
12 Ah, the uproar of many peoples—they roar like the roaring of the seas! The rumbling of nations—they rumble like the rumbling of mighty waters! Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri, akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja! Aa, phokoso la anthu a mitundu ina, akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu!
13 The nations rumble like the rumbling of many waters, but our Father will rebuke them, and they will flee far away, driven before the wind like chaff on the hills, like whirling dust before the storm. Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri, koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula. Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri, ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.
14 At evening, sudden terror! Before morning, they are gone. This is the portion of those who plunder us, the lot of those who loot us. Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika, ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa. Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu, gawo la amene amatibera zinthu zathu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]