Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 16 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Send the lambs to the ruler of the land, from Sela by way of the wilderness, to the mountain of the daughter of Zion. Anthu a ku Mowabu atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa, kuchokera ku Sela kudutsa chipululu mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
2 Like fluttering birds, like a scattered nest, so are the daughters of Moab at the fords of the Arnon. Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku akazimwaza mʼchisa, momwemonso akazi a ku Mowabu akuyendayenda ku madooko a Arinoni.
3 Give counsel; grant justice; make your shade like night at the height of noon. Hide the outcasts; do not betray the fugitive. Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti, “Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite. Inu mutiteteze kwa adani anthu. Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo. Mutibise, musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
4 Let my outcasts dwell among you, Moab; be a shelter to them from the destroyer. When the oppressor is no more, and destruction has ceased, and the tramplers have vanished from the land, Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu; mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.” Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso, kuwononga kudzaleka; waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
5 then a throne will be established in covenant love, and on it will sit in faithfulness, in the tent of David, one who judges and seeks justice and is swift to do righteousness. Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi; mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.
6 We have heard of Moab's pride—how very proud he is—of his arrogance, his pride, and his fury; his boasting is empty. Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri. Kunyada kwawo ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo, zonse ndi zopanda phindu.
7 Therefore let Moab wail for Moab; let everyone wail. Mourn, utterly stricken, for the raisin cakes of Kir-hareseth. Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri; iwo akulirira dziko lawo. Akubuma momvetsa chisoni chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
8 For the fields of Heshbon wither, and the vine of Sibmah; the rulers of the nations have struck down its choice branches, which reached as far as Jazer and strayed into the wilderness; its shoots spread out and crossed over the sea. Minda ya ku Hesiboni yauma, minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga. Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda minda ya mpesa wabwino, imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri, mpaka kutambalalira ku chipululu. Mizu yake inakafika mpaka ku tsidya la nyanja.
9 Therefore I weep with the weeping of Jazer for the vine of Sibmah; I drench you with my tears, Heshbon and Elealeh, for over your summer fruit and your harvest the battle shout has fallen. Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri, chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima. Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali, ndikukunyowetsani ndi misozi! Mwalephera kupeza zokolola, chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
10 Joy and gladness are taken away from the fruitful field, and in the vineyards no songs are sung, no cheers are raised. No one treads out wine in the presses; I have put an end to the shouting. Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso; palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa; palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa, pakuti ndathetsa kufuwula.
11 Therefore my heart moans like a lyre for Moab, my inmost being for Kir-heres. Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu, mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
12 And when Moab presents himself, when he wears himself out on the high place and comes to his sanctuary to pray, he will not prevail. Ngakhale anthu a ku Mowabu apite ku malo awo achipembedzo koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe chifukwa sizidzatheka.
13 This is the word that our Father spoke concerning Moab in the past. Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu.
14 But now our Father has spoken: "In three years, like the years of a hired worker, the glory of Moab will be scorned, in spite of all his great numbers; and the remnant will be very few and feeble." Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]