Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 19 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 An oracle about Egypt. Look—our Father rides a swift cloud into Egypt. Egypt's idols tremble before him, and Egypt's heart melts within. Uthenga onena za Igupto: Taonani, Yehova wakwera pa mtambo waliwiro, ndipo akupita ku Igupto. Mafano a ku Igupto akunjenjemera pamaso pake, ndipo mitima ya Aigupto yachokamo ndi mantha.
2 I will stir up Egypt against Egypt, and they will fight, each against his brother and each against his neighbor, city against city, kingdom against kingdom. “Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha; mʼbale adzamenyana ndi mʼbale wake, mnansi ndi mnansi wake, mzinda ndi mzinda unzake, ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.
3 The spirit of Egypt will be poured out within it, and I will swallow up its counsel; they will inquire of the idols and the spirit-mediums, the ghosts and the necromancers. Aigupto adzataya mtima popeza ndidzalepheretsa zolinga zawo; adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu.
4 I will hand Egypt over into the grip of a harsh master, and a fierce king will rule over them—declares the Father of heaven's armies. Ndidzawapereka Aigupto kwa olamulira ankhanza, ndipo mfumu yoopsa idzawalamulira,” akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
5 The waters of the sea will dry up, and the river will be parched and dry. Madzi a mu mtsinje wa Nailo adzaphwa, ndipo mʼmbali mwa mtsinje mudzangʼaluka ndi kuwuma.
6 The canals will stink; the streams of Egypt will dwindle and dry up; reed and rush will wither. Ngalande zake zidzanunkha; ndipo mitsinje ya Igupto idzayamba kuchepa ndi kuwuma. Bango ndi dulu zidzafota,
7 The bare places along the Nile, at the mouth of the Nile, and everything sown beside the Nile will dry up, blow away, and be no more. ndiponso zomera za mʼmphepete mwa Nailo ndi ku mathiriro a mtsinjewo. Zonse zodzalidwa mʼmbali mwa Nailo zidzawuma, zidzawuluzika ndipo sizidzaonekanso.
8 The fishermen will mourn; all who cast a hook into the Nile will lament, and those who spread nets on the water will waste away. Asodzi adzabuwula ndi kudandaula, onse amene amaponya mbedza mu Nailo; onse amene amaponya makoka mʼmadzi adzalira.
9 The workers in combed flax will be ashamed, and the weavers of white cloth. Amene amagwira ntchito yopota thonje adzataya mtima, anthu oluka nsalu zofewa zabafuta adzataya chiyembekezo.
10 Her weavers will be crushed, and all who work for wages will be sick at heart. Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi, ndipo anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzatheratu mphamvu.
11 The princes of Zoan are nothing but fools; Pharaoh's wisest counselors give senseless counsel. How can you say to Pharaoh, "I am a son of the wise, a son of ancient kings"? Akuluakulu a ku Zowani ndi zitsiru; aphungu a nzeru a Farao amalangiza zopusa. Kodi mungathe kunena bwanji kwa Farao kuti, “Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru, wophunzira wa mafumu akale?”
12 Where now are your wise men? Let them tell you and make known what the Father of heaven's armies has planned against Egypt. Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti? Abweretu kuti akuwuze ndi kukudziwitsa zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonza kuchitira dziko la Igupto.
13 The princes of Zoan have become fools, the princes of Memphis are deceived; the cornerstones of her tribes have led Egypt astray. Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru, atsogoleri a ku Mefisi anamizidwa; atsogoleri a dziko la Igupto asocheretsa anthu a dzikolo.
14 Our Father has poured into her a spirit of confusion, and they have made Egypt stagger in all it does, like a drunkard staggering in his vomit. Yehova wasocheretsa anthu a ku Igupto. Iwo akuchita kudzandira pa zonse zimene akuchita, ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake.
15 There will be nothing Egypt can do, whether head or tail, palm branch or reed. Palibe chimene munthu wa mu Igupto angachite, mtsogoleri kapena wotsatira, nthambi ya kanjedza kapena bango.
16 In that day the Egyptians will be like women—trembling in fear at the hand the Father of heaven's armies raises against them. Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga.
17 The land of Judah will terrify Egypt; all who hear it named will be afraid, because of what the Father of heaven's armies is planning against them. Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto.
18 In that day five cities in Egypt will speak Canaan's language and swear allegiance to the Father of heaven's armies. One will be called the City of the Sun. Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.
19 In that day there will be an altar to our Father in the heart of Egypt, and a pillar to him at its border. Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso.
20 It will be a sign and witness to the Father of heaven's armies in the land of Egypt. When they cry out to our Father because of oppressors, he will send them a savior and defender, and rescue them. Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa.
21 Our Father will reveal himself to Egypt; that day the Egyptians will know him, worship with sacrifice and offering, and make vows to him and fulfill them. Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo.
22 Our Father will strike Egypt—striking and healing. They will return to him; he will hear their pleas and heal them. Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa.
23 In that day a highway will run from Egypt to Assyria. Assyrians will enter Egypt and Egyptians Assyria, and Egypt will worship with Assyria. Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi.
24 That day Israel will be third with Egypt and Assyria, a blessing in the midst of the earth, Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi.
25 for the Father of heaven's armies has blessed them: "Blessed be Egypt my children, Assyria my handiwork, and Israel my inheritance." Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]