Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Nahum 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The scatterer has come up against you, Nineveh. Guard the fortress, watch the road, brace yourself, marshal all your strength! Wodzathira nkhondo akubwera kudzalimbana nawe, Ninive. Tetezani malinga anu, dziyangʼanani ku msewu, konzekerani nkhondo, valani dzilimbe.
2 For our Father is restoring the majesty of Jacob, like the majesty of Israel, though plunderers have stripped them bare and ruined their branches. Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobo ngati ulemerero wa Israeli, ngakhale anthu owononga anawawononga kotheratu ndipo anawononganso mpesa wawo.
3 The shields of his warriors are dyed red, the valiant men are clothed in scarlet; the chariots flash like fire on the day they are made ready, and the spears of cypress are brandished. Zishango za ankhondo ake ndi zofiira; asilikali ake avala zovala zofiirira. Zitsulo za pa magaleta zikunyezimira tsiku la kukonzekera kwake. Akuonetsa mikondo ya mkungudza yonoledwa.
4 The chariots storm through the streets, they rush back and forth in the squares; they look like torches, they dart like lightning. Magaleta akuthamanga mʼmisewu akungothamangathamanga pa mabwalo. Akuoneka ngati miyuni yoyaka; akuthamanga ngati chingʼaningʼani.
5 He summons his officers; they stumble as they march; they hurry to the wall, and the protective shield is set in place. Iye akuyitanitsa asilikali ake wolemekezeka, koma iwo akubwera napunthwa. Akuthamangira ku linga la mzinda; akuyimika chodzitchinjirizira pamalo pake.
6 The river gates are thrown open, and the palace collapses. Atsekula zipata zotchinga madzi a mu mtsinje ndipo nyumba yaufumu yagwa.
7 It is decreed: she is stripped bare and carried away, while her servant girls moan like doves, beating their chests. Zatsimikizika kuti mzinda utengedwa ndi kupita ku ukapolo. Akapolo aakazi akulira ngati nkhunda ndipo akudziguguda pachifuwa.
8 Nineveh is like a pool whose waters are draining away. "Stop! Stop!" they cry, but no one turns back. Ninive ali ngati dziwe, ndipo madzi ake akutayika. Iwo akufuwula kuti, “Imani! Imani!” Koma palibe amene akubwerera.
9 Plunder the silver! Plunder the gold! There is no end to the treasure, an abundance of every precious thing. Funkhani siliva! Funkhani golide! Katundu wake ndi wochuluka kwambiri, chuma chochokera pa zinthu zake zamtengowapatali!
10 Emptiness and desolation and ruin! Hearts melt, knees give way, anguish grips every body, and every face grows pale. Iye wawonongedwa, wafunkhidwa ndipo wavulidwa! Mitima yasweka, mawondo akuwombana, anthu akunjenjemera ndipo nkhope zasandulika ndi mantha.
11 Where now is the lions' den, the feeding place of the young lions, where the lion and lioness prowled, and the lion's cubs, with no one to make them afraid? Kodi tsopano dzenje la mikango lili kuti, malo amene mikango inkadyetserako ana ake, kumene mkango waumuna ndi waukazi unkapitako, ndipo ana a mkango sankaopa kanthu kalikonse?
12 The lion tore enough for his cubs and strangled prey for his lionesses; he filled his lairs with the kill and his dens with torn flesh. Mkango waumuna unkapha nyama yokwanira ana ake ndiponso kuphera nyama mkango waukazi, kudzaza phanga lake ndi zimene wapha ndiponso dzenje lake ndi nyama imene waphayo.
13 "See, I am against you," declares the Father of heaven's armies. "I will send your chariots up in smoke, and the sword will devour your young lions. I will cut off your prey from the earth, and the voice of your messengers will be heard no more." Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikutsutsana nawe. Ndidzatentha magaleta ako mpaka utsi tolotolo, ndipo lupanga lidzapha mikango yako yayingʼono; sindidzakusiyira chilichonse choti udye pa dziko lapansi. Mawu a amithenga anu sadzamvekanso.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]