Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Nahum 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 An oracle concerning Nineveh. The book of the vision of Nahum the Elkoshite. Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.
2 Our Father is jealous and avenging; our Father takes vengeance and is filled with wrath. Our Father takes vengeance on his adversaries, and he reserves his wrath for his enemies. Yehova ndi Mulungu wansanje ndiponso wobwezera; Yehova amabwezera ndipo ndi waukali. Yehova amabwezera adani ake ndipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo.
3 Our Father is slow to anger and great in power, and he will never leave the guilty unpunished. His way is in the whirlwind and the storm, and the clouds are the dust beneath his feet. Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu; ndipo sadzalola kuti munthu wolakwa asalangidwe. Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe, ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake.
4 He rebukes the sea and dries it up; he makes all the rivers run dry. Bashan and Carmel wither, and the blossom of Lebanon fades. Amalamulira nyanja ndipo imawuma; amawumitsa mitsinje yonse. Zomera za ku Basani ndi Karimeli zimawuma ndipo maluwa a ku Lebanoni amafota.
5 The mountains quake before him, and the hills melt away. The earth heaves at his presence—the world and all who live in it. Mapiri amagwedera pamaso pake ndipo zitunda zimasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo.
6 Who can stand before his fury? Who can endure the heat of his anger? His wrath pours out like fire, and the rocks shatter before him. Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa? Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa? Ukali wake ukuyaka ngati moto; matanthwe akunyeka pamaso pake.
7 Our Father is good, a stronghold in the day of trouble; he knows those who take refuge in him. Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,
8 But with an overwhelming flood he will put an end to her place, and he will pursue his enemies into darkness. koma ndi madzi achigumula choopsa Iye adzawononga adani ake (Ninive); adzapirikitsira adani ake ku malo a mdima.
9 What do you plot against our Father? He will put a complete end to it; trouble will not rise up a second time. Chiwembu chilichonse chimene akukonzekera kumuchitira Yehova adzachiwononga kotheratu; msautso sudzabweranso kachiwiri.
10 For though they are entangled like thorns and soaked in their drink, they will be consumed like dry stubble. Iwo adzakodwa mu ziyangoyango za minga ndipo adzaledzera ndi vinyo wawo; adzatenthedwa ngati ziputu zowuma.
11 From you, Nineveh, came one who plots evil against our Father, a counselor of wickedness. Kwa iwe, Ninive, kunachokera munthu wa cholinga choyipa, wofuna kuchitira Yehova chiwembu, amene amapereka uphungu woyipa.
12 This is what our Father says: However strong and numerous they are, they will be cut down and disappear. Though I have made you suffer, I will make you suffer no more. Yehova akuti, “Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi, kaya iwowo ndi ambiri, koma adzawonongedwa ndi kutheratu. Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda, sindidzakuzunzanso.
13 Now I will break his yoke from your neck and tear away your chains. Tsopano ndidzathyola goli lake pa khosi lako ndipo ndidzadula maunyolo ako.”
14 Our Father has commanded about you, Nineveh: your name will have no descendants. I will cut off the carved image and cast idol from your gods' house. I will make your grave—you are contemptible. Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti, “Sudzakhala ndi zidzukulu zimene zidzadziwike ndi dzina lako. Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumba amene ali mʼnyumba ya milungu yako. Ine ndidzakukumbira manda chifukwa ndiwe woyipitsitsa.”
15 Look! There on the mountains, the feet of one who brings good news, who proclaims peace! Celebrate your feasts, Judah; fulfill your vows. For never again will the wicked invade you; they are completely cut off. Taonani, pa phiripo, mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino, amene akulengeza za mtendere! Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu ndipo kwaniritsani malumbiro anu. Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo; iwo adzawonongedwa kotheratu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]