Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Nahum 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Woe to the city of bloodshed, all full of lies and plunder—the prey never departs! Tsoka kwa mzinda wopha anthu, mzinda wodzaza ndi mabodza, mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo, mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse!
2 The crack of the whip, the rumble of wheels, galloping horses, and bounding chariots! Kulira kwa zikwapu, mkokomo wa mikombero, kufuwula kwa akavalo ndiponso phokoso la magaleta!
3 Charging horsemen, flashing swords, glittering spears—a multitude of slain, a heap of corpses, bodies without end; they stumble over the dead. Kuthamanga kwa anthu okwera pa akavalo, kungʼanima kwa malupanga ndi kunyezimira kwa mikondo! Anthu ambiri ophedwa, milumilu ya anthu akufa, mitembo yosawerengeka, anthu akupunthwa pa mitemboyo.
4 All because of the rampant prostitution of this seductive prostitute, the mistress of sorceries, who sells nations through her prostitution and peoples through her sorceries. Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere, wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga, amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake, ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake.
5 "Look, I am against you,' declares the Father of heaven's armies, 'and I will lift your skirts over your face; I will show the nations your nakedness and the kingdoms your shame. Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikutsutsana nawe. Ndidzakuvula chovala chako. Anthu a mitundu ina ndidzawaonetsa umaliseche wako ndipo udzachita manyazi pamaso pa maufumu onse.
6 I will pelt you with filth, treat you with contempt, and make you a spectacle.' Ndidzakuthira zonyansa, ndidzakuchititsa manyazi ndiponso kukusandutsa chinthu choseketsa.
7 And all who see you will flee from you and say, 'Nineveh is laid waste; who will grieve for her?' Where can I find comforters for you?'" Onse amene adzakuona adzakuthawa ndipo adzati, ‘Ninive wasanduka bwinja, adzamulira ndani?’ Kodi ndingamupeze kuti munthu woti nʼkukutonthoza?”
8 Are you better than Thebes, that sat by the Nile with water all around her, whose rampart was the sea, whose wall was the waters? Kodi ndiwe wopambana Tebesi, mzinda wokhala mʼmbali mwa Nailo, wozunguliridwa ndi madzi? Mtsinjewo unali chitetezo chake, madziwo anali linga lake.
9 Cush was her strength, and Egypt without limit; Put and the Libyans were among her allies. Mphamvu zake zinali Kusi ndi Igupto, Puti ndi Libiya anali ena mwa abwenzi ake.
10 Yet she became an exile; she went into captivity. Her infants were dashed to pieces at every street corner. They cast lots for her honored men, and all her great men were bound in chains. Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwa ndipo anapita ku ukapolo. Ana ake anawaphwanyitsa pansi mʼmisewu yonse ya mu mzindamo. Anachita maere ogawana anthu ake otchuka, ndipo anthu ake onse amphamvu anamangidwa ndi maunyolo.
11 You too will be drunk; you will go into hiding; you too will seek refuge from the enemy. Iwenso Ninive udzaledzera; udzabisala ndipo udzafunafuna malo othawirako kuopa mdani.
12 All your fortresses are like fig trees with the first-ripe figs—when shaken, they fall into the mouth of the eater. Malo ako onse otetezedwa ali ngati mitengo ya mkuyu yokhala ndi zipatso zoyambirira kucha; pamene agwedeza mitengoyo, nkhuyuzo zimagwera mʼkamwa mwa wofuna kuzidya.
13 Look, your troops are women in your midst. The gates of your land are flung wide open to your enemies; fire has devoured your bars. Tayangʼana ankhondo ako, onse ali ngati akazi! Zipata za dziko lako zatsekukira adani ako; moto wapsereza mipiringidzo yake.
14 Draw water for the siege; strengthen your fortresses; go into the clay and tread the mortar; take hold of the brick mold! Tungani madzi woti mudzamwe nthawi ya kuzunguliridwa kwanu, limbitsani chitetezo chanu! Pondani dothi, ikani mʼchikombole, konzani khoma la njerwa!
15 There the fire will devour you; the sword will cut you down; it will consume you like the young locust. Multiply yourselves like the young locust; multiply like the swarming locust! Kumeneko moto udzakupserezani; lupanga lidzakukanthani ndipo lidzakuwonongani ngati likuwononga ziwala. Chulukanani ngati ziwala, chulukanani ngati dzombe!
16 You multiplied your merchants more than the stars of the heavens. The young locust strips the land and flies away. Mwachulukitsa chiwerengero cha anthu a malonda anu mpaka kupambana nyenyezi za mlengalenga, koma iwo ngati dzombe akuwononga dziko ndipo kenaka akuwuluka nʼkuchoka.
17 Your guards are like locusts, and your officials like clouds of locusts that settle on the walls on a cold day—when the sun rises, they fly off, and no one knows where they are. Akalonga ako ali ngati dzombe, akuluakulu ako ali ngati gulu la dzombe limene lamatirira pa khoma nthawi yozizira, koma pamene dzuwa latuluka limawuluka, ndipo palibe amene amadziwa komwe lapita.
18 Your shepherds are asleep, king of Assyria; your nobles lie down. Your people are scattered across the mountains, with no one to gather them. Iwe mfumu ya ku Asiriya, abusa ako agona tulo; anthu ako olemekezeka amwalira. Anthu ako amwazikira ku mapiri popanda ndi mmodzi yemwe wowasonkhanitsa.
19 There is no relief for your injury; your wound is fatal. All who hear the news of you clap their hands over you—for who has not felt your endless cruelty pass over them again and again? Palibe chimene chingachize bala lako; chilonda chako sichingapole. Aliyense amene amamva za iwe amawomba mʼmanja chifukwa cha kugwa kwako, kodi alipo amene sanazilawepo nkhanza zako zosatha?
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]