Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 62 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Dzina Latsopano la Ziyoni

1Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete,chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete,mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala,ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.

2Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondondipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.Adzakuyitanira dzina latsopanolimene adzakupatse ndi Yehova.

3Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova,ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.

4Sadzakutchanso “Wosiyidwa,”ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.”Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.”Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.”Chifukwa Yehova akukondwera nawe,ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.

5Monga mnyamata amakwatira namwali,momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira;monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi,chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.

6Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndayikapo alonda;sadzakhala chete usana kapena usiku.Inu amene mumakumbutsa Yehova za malonjezo akemusapumule.

7Musamupatse mpata wopuma mpaka atakhazikitsa Yerusalemukukhala mzinda umene dziko lapansi lidzawutamande.

8Yehova analumbira atakweza dzanja lake.Anati,“Sindidzaperekanso tirigu wakokuti akhale chakudya cha adani ako,ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako watsopanopakuti unamuvutikira.

9Koma amene amakakolola ndiwo amene adzadye buledindi kutamanda Yehova,ndipo amene amasonkhanitsa pamodzi mphesa ndiwo amene adzamwe vinyomʼmabwalo a Nyumba yanga.”

10Tulukani, dutsani pa zipata!Konzerani anthu njira.Lambulani, lambulani msewu waukulu!Chotsani miyala.Kwezani mbendera kuti mitundu ya anthu izione.

11Yehova walengezaku dziko lonse lapansi kuti,Awuzeni anthu a ku Yerusalemu kuti,“Taonani, chipulumutso chanu chikubwera;Yehova akubwera ndi mphotho yakeakubwera nazo zokuyenerani.”

12Iwo adzatchedwa Anthu Opatulika,owomboledwa a Yehova;ndipo adzakutchani “Okondwa a Yehova”“Mzinda umene Yehova sanawusiye.”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]