Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 61 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Uthenga Wabwino wa Yehova

1Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,chifukwa Yehova wandidzozakuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulundiponso kuti ndikamasule a mʼndende.

2Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.Wandituma kuti ndikatonthoze olira.

3Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,nkhata ya maluwa yokongolamʼmalo mwa phulusa,ndiwapatse mafuta achikondwereromʼmalo mwa kulira.Ndiwapatse chovala cha matamandomʼmalo mwa mtima wopsinjika.Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,yoyidzala Yehovakuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.

4Adzamanganso mabwinja akale a mzindandipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso.Adzakonzanso mizinda imene inapasuka,imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.

5Anthu achilendo adzakutumikirani; adzazidyetsa ziweto zanu;iwo adzagwira ntchito mʼminda yanu ya mpesa.

6Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova,adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu.Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu,ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.

7Chifukwa manyazi awo anali owirikiza;ndi kuti munalandirachitonzo ndi kutukwana,adzakondwera ndi cholowa chawo,tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza,ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.

8“Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo;ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa.Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirikandikupangana nawo pangano losatha.

9Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthundipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina.Aliyense wowaona adzazindikirakuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”

10Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova;moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga.Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso,ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo.Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake,ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.

11Monga momwe nthaka imameretsa mbewundiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala,momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamandopamaso pa mitundu yonse ya anthu.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]