Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Hosea 8 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Israeli Akolola Kamvuluvulu

1“Ika lipenga pakamwa pako.Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehovachifukwa anthu aphwanya pangano langandiponso agalukira lamulo langa.

2Israeli akulirira kwa Ine kuti,‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’

3Koma Israeli wakana zabwino;mdani adzamuthamangitsa.

4Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga.Amasankha akalonga popanda chilolezo changa.Amadzipangira mafanoasiliva ndi agolidekoma adzawonongeka nawo.

5Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe!Mkwiyo wanga wayakira anthuwo.Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?

6Mafanowa ndi ochokera ku Israeli!Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso;si Mulungu amene anamupanga.Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa,mwana wangʼombe wa ku Samariya.

7“Aisraeli amadzala mphepondipo amakolola kamvuluvulu.Tirigu alibe ngala;sadzabala chakudya.Akanabala chakudyaalendo akanadya chakudyacho.

8Israeli wamezedwa,tsopano ali pakati pa anthu a mitundu inangati chinthu cha chabechabe.

9Pakuti iwo anapita ku Asiriyangati mbidzi yongodziyendera pa yokha.Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.

10Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu,Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi.Iwo adzayamba kuzunzika pansi paulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.

11“Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo,maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.

12Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga,koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.

13Amapereka nsembe za nyama kwa Inendipo iwo amadya nyamayo,koma Yehova sakondwera nazo.Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawondi kuwalanga chifukwa cha machimo awo:iwowo adzabwerera ku Igupto.

14Israeli wayiwala Mlengi wakendipo wamanga nyumba zaufumu;Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga.Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo,moto umene udzatenthe malinga awo.”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]