Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Hosea 8 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Put the trumpet to your lips! An eagle swoops over my house, because they have broken my covenant and rebelled against my law. “Ika lipenga pakamwa pako. Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova chifukwa anthu aphwanya pangano langa ndiponso agalukira lamulo langa.
2 To me they cry, "My Father! We know you—we, Israel!" Israeli akulirira kwa Ine kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’
3 Israel has rejected what is good; an enemy will pursue him. Koma Israeli wakana zabwino; mdani adzamuthamangitsa.
4 They set up kings, but not from me; they appointed princes, and I knew nothing of it. With their silver and gold they made themselves idols, only to be cut off. Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amasankha akalonga popanda chilolezo changa. Amadzipangira mafano asiliva ndi agolide koma adzawonongeka nawo.
5 I have rejected your calf, Samaria; my anger burns against them. How long will they be incapable of innocence? Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe! Mkwiyo wanga wayakira anthuwo. Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?
6 For this calf is from Israel; a craftsman made it—it is not God. The calf of Samaria will be broken to pieces. Mafanowa ndi ochokera ku Israeli! Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso; si Mulungu amene anamupanga. Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa, mwana wangʼombe wa ku Samariya.
7 They sow the wind, and they will reap the whirlwind. The standing grain has no heads; it yields no flour. And if it were to yield, foreigners would swallow it down. “Aisraeli amadzala mphepo ndipo amakolola kamvuluvulu. Tirigu alibe ngala; sadzabala chakudya. Akanabala chakudya alendo akanadya chakudyacho.
8 Israel is swallowed up; now they are among the nations like a pot no one wants. Israeli wamezedwa, tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina ngati chinthu cha chabechabe.
9 For they have gone up to Assyria—a wild donkey wandering off alone. Ephraim has hired itself out to lovers. Pakuti iwo anapita ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha. Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.
10 Even though they hire allies among the nations, now I will gather them up. And they will soon writhe under the burden of the king of princes. Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu, Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi. Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.
11 Because Ephraim multiplied altars for sinning, they have become altars for sinning to him. “Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo, maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.
12 Though I wrote out for him the countless things of my law, they were treated as something strange. Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga, koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.
13 As for the sacrifices they offer me, they sacrifice meat and eat it, but I take no delight in them. Now I will remember their guilt and punish their sins; they will return to Egypt. Amapereka nsembe za nyama kwa Ine ndipo iwo amadya nyamayo, koma Yehova sakondwera nazo. Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo: iwowo adzabwerera ku Igupto.
14 Israel has forgotten his Maker and built palaces; and Judah has multiplied fortified cities. But I will send fire on his cities, and it will devour Judah's strongholds. Israeli wayiwala Mlengi wake ndipo wamanga nyumba zaufumu; Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga. Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo, moto umene udzatenthe malinga awo.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]