Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Hosea 4 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Hear the word of our Father, children of Israel, for he has a case against the inhabitants of the land: there is no faithfulness, no covenant love, and no knowledge of him in the land. Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova, chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu amene mumakhala mʼdzikoli: “Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi mulibe kulabadira za Mulungu.
2 There is only swearing and lying, murder and stealing and adultery; they break all bounds, and bloodshed follows bloodshed. Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha. Kuba ndi kuchita chigololo; machimo achita kunyanya ndipo akungokhalira kuphana.
3 Therefore the land mourns, and all who live in it waste away, together with the wild animals and the birds in the sky; even the fish in the sea are swept away. Chifukwa chake dziko likulira ndipo onse amene amakhalamo akuvutika; zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.
4 Yet let no one accuse, let no one lay blame, for your people are like those who quarrel with the priest. “Koma wina asapeze mnzake chifukwa, wina aliyense asayimbe mlandu mnzake, pakuti anthu ako ali ngati anthu amene amayimba mlandu wansembe.
5 You stumble by day, and the prophet stumbles with you by night; and I will destroy your mother. Mumapunthwa usana ndi usiku ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi. Choncho ndidzawononga amayi anu.
6 My people are destroyed for lack of knowledge. Because you have rejected knowledge, I reject you as my priest; because you have forgotten the law of your Father, I also will forget your children. Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa. “Pakuti mwakana kudziwa, Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga; chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu, Inenso ndidzayiwala ana anu.
7 The more they increased, the more they sinned against me; I will turn their glory into shame. Ansembe ankati akachuluka iwo ankandichimwiranso kwambiri; iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.
8 They feed on the sin of my people and set their hearts on their wrongdoing. Amalemererapo pa machimo a anthu anga ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azipitiriza kuchimwa.
9 So it will be: like people, like priest. I will punish them for their ways and repay them for their deeds. Ndipo zidzakhala motere: zochitikira anthu ena, zidzachitikiranso ansembe. Ndidzawalanga onsewo chifukwa cha njira zawo, ndidzawabwezera chifukwa cha machitidwe awo.
10 They will eat but not be satisfied; they will give themselves to prostitution but not multiply, because they have forsaken our Father and abandoned his ways. “Iwo azidzadya koma sadzakhuta; azidzachita zachiwerewere koma sadzachulukana, chifukwa anasiya Yehova kuti adzipereke
11 Prostitution, wine, and new wine take away good sense. ku zachiwerewere, ku vinyo wakale ndi watsopano, zimene zimachotsa nzeru zomvetsa zinthu
12 My people consult a piece of wood, and their staff gives them oracles; for a spirit of prostitution has led them astray, and they have played the prostitute, forsaking their Father. za anthu anga. Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha. Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa; iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo.
13 They sacrifice on the mountaintops and burn offerings on the hills, under oak, poplar, and terebinth, because their shade is pleasant. So your daughters turn to prostitution and your brides to adultery. Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri ndi kufukiza lubani pa zitunda, pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi, pamene pali mthunzi wabwino. Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.
14 I will not punish your daughters when they turn to prostitution, nor your brides when they commit adultery; for the men themselves go off with prostitutes and offer sacrifices with the temple prostitutes—a people without understanding comes to ruin. “Ine sindidzalanga ana anu aakazi pamene iwo adzachita zachiwerewere, kapena akazi a ana anu pamene adzachita zigololo. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako. Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!
15 Though you, Israel, play the prostitute, let Judah not become guilty. Do not go to Gilgal; do not go up to Beth-aven; and do not swear, 'As surely as our Father lives.' “Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli, Yuda asapezeke ndi mlandu wotere. “Usapite ku Giligala. Usapite ku Beti-Aveni. Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’
16 Israel is stubborn, like a stubborn heifer. Can our Father now pasture them like a lamb in an open meadow? Aisraeli ndi nkhutukumve, ngosamva ngati ana angʼombe. Kodi Yehova angathe kuwaweta bwanji ngati ana ankhosa pa msipu wabwino?
17 Ephraim is joined to idols; leave him alone. Efereimu waphathana ndi mafano; mulekeni!
18 When their drink is gone, they give themselves to prostitution; their rulers dearly love disgrace. Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha, amapitiriza kuchita zachiwerewere; atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi.
19 A wind has wrapped them in its wings, and they will be ashamed because of their altars. Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]