1Mmeneyo Melikizedeki wadali mfumu wa ku mujhi wa Salemu, ni mjhukulu wa Mnungu uyo wali kumwamba kupunda. Ibulahimu yapo wamabwela kuchokela kunghondo, uko wadaapa mafumu, Melikizedeki wadapezana naye, wadampembha Mnungu wamchitile vabwino,2Niiye Ibulahimu wadampacha malo ya khumi ya vindhu vonjhe ivo wadalinavo. Mate yoyamba ya jhina Melikizedeki, “Mfumu uyo walamulila kwa kuchita vabwino,” ni ndande iye wadali mfumu wa kumujhi wa Selemu mujhi umenewo mate yake ni, “Mfumu wa mtendele.”3Tate wake ni mayi wake sachulidwa kapina khamu lake silichulidwa ni silidalembedwe kuti wadabadwa liti, kapina wadamwalila liti, walingati mwana wa Mnungu, ni wayendekela kukhala Mjhukulu muyaya.
4Chipano muona mundhu uyu umo wadali wamkulu. Ambuye wathu Ibulahimu wadampacha malo ya kumi ya vindhu vonjhe ivo wadavikusa kunghondo.5Tijhiwa kuti kuchokana ni thauko, mibadwa ya Lawi yawo ali ajhukulu, ifunika atenge malo ya khumi kuchokela kwa wandhu, ingakhale achabale wao. Idafuka achite chimwecho ata ngati wonjhe ni mibadwa ya Ibulahimu.6Nambho Melikizedeki mmeneyo siwadali wa khamu la Lawi. Ata chimwecho wadalandila malo ya khumi kuchokela kwa Ibulahimu, ni wadampacha mwawi iye wadakambidwa ni Mnungu kuti siwapachidwe mwawi.7Palibe kukhaikila ata pang'ono kuti uyo waapacha mwawi wandhu ni wamkulu kupitilila yujha wapachidwa mwawi.8Chinchijhanjho ajhukulu alandila malo ya kumi ni wandhu amwalila, nambho pano Melikizedeki uyo walandila malo ya khumi, ikambika kuti siwamwalila.9Chimwecho tikhoza kukamba kuti, Lawi uyo mibadwa yake ilandila malo ya kumi, niiye wadachocha malo yakumi pajha Ibulahimu wadachocha malo ya khumi kwa Melikizedi.10Pakuti Melikizedeki yapo wadapezana ni Ibilahimu Lawi wadali wakali siwadabadwe, ndekuti kukamba Lawi wadali mthupi la ambuyake Ibulahimu.
11Ingakale ujhukulu wa Lawi, udachata thauko la Musa ata chimwecho ujhukulu umenewo siudakwane. Ndande imeneyo, umafunika ujhukulu wina ngati ujhukulu wa Melikizedeki, uwo siuli ngati wa Aloni.12Pakuti ujhukulu ukang'anamuka, ifunika ni thauko nalo ling'anamuke.13Ambuye wathu Yesu akambidwa pa vindhu ivi, wadali wa khamu lina ni palibe mundhu wa khamu lake uyo wadachita njhito ya ujhukulu.14Ijhiwika kuti iye wadabadwa pa fuko la Yuda ilo Musa siwadalichulepo yapo wamakamba nghani za ujhukulu.
Mjhukulu mwina
15Nichindhu ichi chijhiwika kupunda, mjhukulu mwina uyo wali ngati mjhukulu Melikizedeki wathochokela.16Yesu siwadachitike mjhukulu kwa thauko ni maagizo ya wandhu, nambho kwa mbhavu ya umoyo wake uwo ulibe pothela.17Pakuti yalembedwa mamalembo kuti, “Iwe ni mjhukulu muyaya, ngati umo wadali mjhukulu Melikizedeki.”18Chipano lijha thauko la kale lidafutidwa ndande lidali lofooka ni siimafunike.19Pakuti thauko la Musa silidakhoze kumchita mundhu siwadachita vindhu voipa. Nambho chipano, pamalo pake Mnungu watipelekela chindhu chabwino icho tichiyembekeza icho kwa chimenecho tikhoza kumuwandikila Mnungu.
20Kupitilila chindhu cha bwino icho tichiyembekeza tili ni lumbilo la Mnungu. Ndhawi iyo Alawi amachitidwa kukhala ajhukulu Mnungu siwadalumbile.21Nambo Yesu wadachitidwa mjhukulu kwa kulumbila, yapo Mnungu wadamkambila,“Ambuye alumbila,nisiang'anamula maganizo yao,‘Iwe ni mjhukulu muyaya.’”
22Basi kuchokana ni kulumbila kumeneko, Yesu nde uyo wachita chipangano cha bwino kupunda chikwanile.
23Niamenewo ajhukulu wina adali ambili ndande adamwalila ni sadakhoze kuyendekela ni njhito yawo.24Nambho Yesu osati ngati anyiiwo, iye siwakhale mjhukulu muyaya.25Chimwecho iye siku zonjhe wakhoza kwaombola wonjhe ampitila Mnungu kwa kumkhulupilila, pakuti iye wakhala muyaya ni wapembhela kwa Mnungu ndhawi zonjhe.
26Basi chidali chindhu chofunika kupunda kwathu kukhala ni mjhukulu ngati mneneyo, wavomelezeka ni Mnungu ni uyo walibe cholakwa kapina machimo mkati mwake, ni Mnungu wampatula patali ni wandhu amachimo ni wamkweza kumwamba kupitilila mlengalenga.27Ajhukulu adafunika kuchocha mahoka ndande ya machimo yawo ni machimo ya wandhu wina ni amchita chimwecho mala za mbili. Nambho Yesu wadajhichocha pamtanda mala kamojhipe ndande ya machimo ya wandhu wonjhe ni siwadafunike kubwelelanjho.28Kuchokana ni thauko la Musa wandhu amaikidwa kukhala ajhukulu wakulu, ingakhale sadakwanile. Nambho vyaka vambili pambuyo pa thauko la Musa, Mnungu wadalumbila ndhawi iyo wama muika mwana wake kukhala mjhukulu wamkulu okwanila muyaya.
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved. Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]
Read offline
Save NTNYBL2025 on this device and read it with no connection. Downloads stay in this browser or app only.