Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 6 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Chipano tisidaendekela ni mayaluzo ya mmayambo yayo yakambilila nghani za Kilisito, nambho tiendekele mchogolo ni mayaluzo yokhwima. Ni asati kuyendekela kukambilila mayaluzo ya ukhalo uwo siumkwadilicha Mnungu ni chikhulupi, 2mayaluzo ya kubatiza ni nikupembhela kwa kuikila manja, kuhyukichidwa ni lamulo la muyaya. 3Yameneyo sitiyachite Mnungu wakakonda.

4Pakuti wandhu yawo adathoujhiwa uzene wa Mnungu ni kuzijhiwa mbhaso za kumwamba kwa Mnungu ni adalandila Mzimu Woyela, 5ni adajhiwa ubwino wa mawu la Mnungu ni kuujhiwa nghani za mbhavu za jhiko ilo likujha, 6pambuyo adasiya kumkhulupilila Mnungu, siikhozeka kwabweza wandhu achamenewo kuti alape machimo yawo ni kuyasiyanjho. Achamenewo achita dala kumpachikanjho pamtanda mwana wa Mnungu ni kumlengecha njhoni pandhandala.

7Ndhaka iyo ilandila vula iyo iinyela tetete ni kupukicha mimela iyo impacha phindhu mlimi, ndhaka imeneyo yapachidwa mwawi ni Mnungu. 8Nambho ndhaka ikamela mitengo ya minga ni machangale, ilibe phindu, ili pafupi siilesedwe ni Mnungu ni mathelo yake kubuchidwa moto.

9Ingakhale tikamba kwa mtundu uwu achabale wathu yawo tikukondani, nambho tijhiwa zenedi kuti mchita vindhu vabwino kupunda, ivo vilangiza kuti anyiimwe mwaomboledwa ni Mnungu. 10Mnungu walamula popande kukondelela, siwaiyawalila njhito yanu iyo mwaichita, kapina chikondi icho mwachilangiza ndande yake, kwa kupitila kwathangatila wokhulupilila achanjanu, kuyambila mmayambo mbaka chipano. 11Khumbilo lathu ni kuti kila mmojhi wanu waendekele kuchita chimwecho mbaka pothela, dala yajha muyalindila mkhoze kuyalandila. 12Chimwecho, simdakhala alesi, nambho mkhale ngati wajha akhulupilila ni yawo alimbamtima, chimwecho adalandila yajha wadakamba Mnungu kuti siwapache.

Icho wakamba Mnungu ni chauzene

13Mnungu yapo wadakamba kuti wadakampacha chindhu Ibulahimu, wadalumbila kwa jhina lake mwene, pakuti padalibe waliyonjhe uyo wadali wamkulu kupitilila iye. 14Mnungu wadakamba, “Zenedi sinikupache mwawi ni sinikupache mibadwa yambili.” 15Ibulahimu wadalindila kwa kulimbilamtima, ni mchimwecho wadalandila chijha chindhu wadakamba Mnungu kuti siwampache. 16Wandhu yapo alumbila, alumbila kwa jhina la iye wali wamkulu kupitilila anyiiwo, ni kulumbila kwawo kumaliza mitafu yawo yonjhe. 17Chimwecho Mnungu wadalumbila dala kwachimikizila wajha wandhu yawo Mnungu wadakamba kuti siwapache siyang'anamukadi. 18Chipano kuli vindhu viwili ivo sivikhoza kung'anamika ni ivo Mnungu siwakoza kukamba unami, vindhu vimenevo ni chijha wadachikamba ni kulumbila kwake, ife tamthawila iye dala tiyendekele kusangalala, tithilidwa mtima dala tiyendekele kuyembekeza yajha yaikidwa pachogolo pathu. 19Kuyembekeza kumeneko kutichita tisangalale ni tikhale ambhavu ngati ndondowe umo igwililila Sitima. Niuyo timuembeza ni Yesu, uyo wapita mbaka kupaziya la nyumba ya mnungu ya kumwamba ni kulowa mbaka pamalo poyela kupunda. 20Yesu mwene wachogolela kulowa mnenemo mmalo mwathu, ni wakhala mjhukulu wamkulu muyaya ngati umo wadali mjhukulu Melikizedeki.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]