Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 64 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Oh, that you would tear open the heavens and come down, that the mountains would quake at your presence, Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!
2 as fire sets brushwood ablaze and causes water to boil—to make your name known to your adversaries, so that the nations would tremble at your presence! Monga momwe moto umatenthera tchire ndiponso kuwiritsa madzi, tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu, ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.
3 When you did awesome things that we did not expect, you came down, and the mountains quaked at your presence. Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere, ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.
4 Since ancient times, no one has heard or perceived by ear, no eye has seen any besides you, who acts for the one who waits for him. Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo kapena kuona Mulungu wina wonga Inu, amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.
5 You welcome those who gladly do what is right, who remember you as they walk in your ways. But you were angry, and we sinned; we have long been in our sins—can we be saved? Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama, amene amakumbukira njira zanu. Koma Inu munakwiya, ife tinapitiriza kuchimwa. Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
6 We have all become like one who is unclean, and all our righteous deeds are like a filthy garment. We all wither like a leaf, and our sins, like the wind, sweep us away. Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa, ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo; tonse tafota ngati tsamba, ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
7 There is no one who calls on your name, who rouses himself to take hold of you; for you have hidden your face from us and have handed us over to our sins. Palibe amene amapemphera kwa Inu kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu; pakuti mwatifulatira ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.
8 But now, you are our Father; we are the clay, and you are our potter; we are all the work of your hand. Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu. Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba; ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
9 Do not be so terribly angry, our Father, and do not remember our sin forever. Look, please—we are all your people. Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso musakumbukire machimo athu mpaka muyaya. Chonde, mutiganizire, ife tikupempha, pakuti tonsefe ndi anthu anu.
10 Your holy cities have become a wilderness; Zion has become a wilderness, Jerusalem a desolation. Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu; ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.
11 Our holy and beautiful house, where our fathers praised you, has been burned with fire, and all that we treasured has become a ruin. Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani, yatenthedwa ndi moto ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.
12 After all this, will you hold back, our Father? Will you keep silent and afflict us so terribly? Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza? Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]