Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 65 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 I let myself be sought by those who did not ask for me; I let myself be found by those who did not seek me. I said, "Here I am, here I am," to a nation that did not call on my name. “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu; ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze. Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine, ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’
2 All day long I have spread out my hands to a rebellious people, who walk in a way that is not good, following their own schemes, Tsiku lonse ndatambasulira manja anga anthu owukira aja, amene amachita zoyipa, natsatira zokhumba zawo.
3 a people who provoke me to my face continually, sacrificing in gardens and burning incense on bricks; Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsa mopanda manyazi. Iwo amapereka nsembe mʼminda ndi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.
4 who sit among the tombs and spend the night in secret places; who eat the flesh of pigs, with broth of forbidden things in their pots; Amakatandala ku manda ndipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika. Amadya nyama ya nkhumba, ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.
5 who say, "Keep to yourself, do not come near me, for I am holier than you." These are smoke in my nostrils, a fire that burns all day long. Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire, chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’ Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga, ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
6 Look, it stands written before me: I will not keep silent, but I will repay; I will repay into their lap, “Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo; sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthu chifukwa cha machimo awo
7 both your own sins and the sins of your ancestors together, says our Father; because they burned incense on the mountains and insulted me on the hills, I will measure into their lap full payment for their former deeds. ndi a makolo awo,” akutero Yehova. “Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo, Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata zimene anachita kale.”
8 This is what our Father says: As the new wine is found in the cluster, and someone says, "Do not destroy it, for there is a blessing in it," so I will do for the sake of my servants, and not destroy them all. Yehova akuti, “Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo, popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’ Inenso chifukwa cha mtumiki wanga; sindidzawononga onse.
9 "I will bring forth descendants from Jacob, and from Judah an heir of my mountains; my chosen will inherit it, and my servants will dwell there. Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo, ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo. Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi, ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.
10 Sharon will become a pasture for flocks, and the Valley of Achor a resting place for herds, for my people who have sought me. Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa, ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombe kwa anthu anga ondifunafuna Ine.
11 But you who forsake me, who forget my holy mountain, who set a table for Fortune and fill cups of mixed wine for Destiny. “Koma inu amene mumasiya Yehova ndi kuyiwala phiri langa lopatulika, amene munamukonzera Gadi chakudya ndi kuthirira Meni chakumwa,
12 I will destine you for the sword, and all of you will bow down to the slaughter, because I called and you did not answer, I spoke and you did not listen; you did what was evil in my eyes and chose what gave me no delight." ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe, ndipo nonse mudzaphedwa; chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani, ndinayankhula koma simunamvere. Munachita zoyipa pamaso panga ndipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.”
13 Therefore this is what the Sovereign Father says: Look, my servants will eat, but you will go hungry; my servants will drink, but you will go thirsty; my servants will rejoice, but you will be put to shame; Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, “Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; atumiki anga adzakondwa, koma inu mudzakhala ndi manyazi.
14 "look, my servants will sing for gladness of heart, but you will cry out for pain of heart and wail for a broken spirit. Atumiki anga adzayimba mosangalala, koma inu mudzalira kwambiri chifukwa chovutika mu mtima ndipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima.
15 You will leave your name to my chosen as a curse, and the Sovereign Father will put you to death; but his servants he will call by another name, Anthu anga osankhidwa adzatchula dzina lanu potemberera. Ambuye Yehova adzakuphani, koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.
16 so that whoever invokes a blessing in the land will bless himself by the Father of truth, and whoever takes an oath in the land will swear by the Father of truth; for the former troubles are forgotten and hidden from my eyes. Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomo adzachita zimenezo kwa Mulungu woona; ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomo adzalumbira mwa Mulungu woona. Pakuti mavuto akale adzayiwalika ndipo adzachotsedwa pamaso panga.
17 "For look, I am creating new heavens and a new earth, and the former things will not be remembered or come to mind. “Taonani, ndikulenga mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukika, zidzayiwalika kotheratu.
18 But be glad and rejoice forever in what I am creating; for look, I am creating Jerusalem to be a joy, and her people to be a gladness. Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya chifukwa cha zimene ndikulenga, pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
19 I will rejoice over Jerusalem and be glad in my people; no longer will the sound of weeping be heard in her, or the cry of distress. Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga. Kumeneko sikudzamvekanso kulira ndi mfuwu wodandaula.
20 No more will there be in it an infant who lives only a few days, or an old man who does not live out his years; for the young man will die one hundred years old, and the one who falls short of one hundred will be thought accursed. “Ana sadzafa ali akhanda ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse. Wamngʼono mwa iwo adzafa ali ndi zaka 100. Amene adzalephere kufika zaka 100 adzatengedwa kukhala wotembereredwa.
21 They will build houses and live in them; they will plant vineyards and eat their fruit. Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo, adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
22 They will not build for another to live in, or plant for another to eat; for my people's days will be like the days of a tree, and my chosen will long enjoy the work of their hands. Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo, kapena kudzala ndi ena nʼkudya. Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo wautali ngati mitengo. Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito ya manja awo nthawi yayitali.
23 They will not labor in vain or bear children for sudden terror, for they are the offspring of those our Father has blessed, and their descendants with them. Sadzagwira ntchito pachabe kapena kubereka ana kuti aone tsoka; chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova, iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.
24 Before they call, I will answer; while they are still speaking, I will hear." Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe. Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.
25 The wolf and the lamb will graze together, and the lion will eat straw like the ox, but dust will be the serpent's food. They will not harm or destroy anywhere on my holy mountain, says our Father. Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ngʼombe, koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala chinthu chopweteka kapena chowononga,” akutero Yehova.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]