Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 63 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Who is this coming from Edom, in crimson-stained garments from Bozrah, this one majestic in his apparel, striding in his great strength? "It is I, proclaiming righteousness, mighty to save." Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu, atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira? Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola, akuyenda mwa mphamvu zake? “Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamo ndiponso wamphamvu zopulumutsa.”
2 Why is your apparel red, and your garments like one who treads in the winepress? Nanga bwanji zovala zanu zili psuu, ngati za munthu wofinya mphesa?
3 "I have trodden the winepress alone, and from the peoples no one was with me; I crushed them in my anger and trampled them in my wrath; their lifeblood splattered on my garments, and I stained all my apparel. “Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa, palibe ndi mmodzi yemwe anali nane. Ndinawapondereza ndili wokwiya ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali; magazi awo anadothera pa zovala zanga, ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.
4 For the day of reckoning was in my heart, and the year of my redeemed had come. Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga; ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika.
5 I looked, but there was no one to help; I was appalled that no one upheld me; so my own arm brought me salvation, and my wrath upheld me. Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza. Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza; choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga, ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.
6 I trampled the peoples in my anger; I made them drunk in my wrath, and I poured out their lifeblood on the ground." Ndinapondereza mitundu ya anthu ndili wokwiya; ndipo ndinawasakaza ndipo ndinathira magazi awo pansi.”
7 I will tell of the covenant love of our Father, the praises of him, according to all that he has done for us, and the great goodness he has shown to the house of Israel, according to his compassion, according to his abundant covenant love. Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova, ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa. Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira. Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake Yehova wachitira nyumba ya Israeli zinthu zabwino zambiri.
8 For he said, "Surely they are my people, children who will not be false." And he became their Savior. Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga, ana anga amene sadzandinyenga Ine.” Choncho anawapulumutsa.
9 In all their affliction he was afflicted, and the messenger of his presence saved them; in his love and in his compassion he redeemed them; he lifted them up and carried them all the days of old. Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse, ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa. Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa, anawanyamula ndikuwatenga kuyambira kale lomwe.
10 But they rebelled and grieved his Holy Spirit; so he turned and became their enemy, and he himself fought against them. Komabe iwo anawukira ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera. Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo ndipo Iye mwini anamenyana nawo.
11 Then he recalled the days of old, of Moses and of his people. Where is the one who led them up from the sea, with his flock's shepherds? Where is the one who placed his Holy Spirit among them, Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana, masiku a Mose mtumiki wake; ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja, pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo? Ali kuti Iye amene anayika Mzimu Woyera pakati pawo?
12 who stretched out his glorious arm at the right hand of Moses, who divided the waters before them to make for himself an everlasting name, Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,
13 who led them through the depths? Like a horse in the wilderness, they did not stumble. amene anawayendetsa pa nyanja yozama? Monga kavalo woyendayenda mʼchipululu, iwo sanapunthwe;
14 Like livestock that go down into the valley, the Spirit of our Father gave them rest. So you led your people, to make for yourself a glorious name. Mzimu Woyera unawapumulitsa ngati mmene ngʼombe zimapumulira. Umu ndi mmene Inu munatsogolera anthu anu kuti dzina lanu lilemekezeke.”
15 Look down from heaven and see, from your holy and glorious dwelling. Where are your zeal and your mighty deeds? The stirring of your heart and your compassion are held back from me. Inu Yehova amene muli kumwambako, pa mpando wanu wolemekezeka, wopatulika ndi waulemerero, tiyangʼaneni ife. Kodi changu chanu ndi mphamvu zanu zili kuti? Simukutionetsanso kukoma mtima kwanu ndi chifundo chanu.
16 For you are our Father, though Abraham does not know us and Israel does not acknowledge us; you are our Father; our Redeemer from ages past is your name. Koma Inu ndinu Atate athu, ngakhale Abrahamu satidziwa kapena Israeli kutivomereza ife; Inu Yehova, ndinu Atate athu, kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu.
17 Why, our Father, do you let us wander from your ways and harden our heart, so that we do not fear you? Return for the sake of your servants, the tribes of your heritage. Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu? Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso? Bwererani chifukwa cha atumiki anu; mafuko a anthu amene ali cholowa chanu.
18 For a little while your holy people held possession; our enemies have trampled your sanctuary. Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa, adani athu anasakaza malo anu opatulika.
19 We have become like those you have never ruled, like those not called by your name. Ife tili ngati anthu amene simunawalamulirepo ngati iwo amene sanakhalepo anthu anu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]