Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 31 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Woe to those who go down to Egypt for help, who rely on horses, who trust in chariots because they are many and in horsemen because they are very strong—but they do not look to the Holy One of Israel, our Father, nor seek him. Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo, amene amadalira akavalo, nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo, koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli, kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.
2 Yet he too is wise and brings disaster; he does not take back his words. He will rise against the house of the evildoers and against the help of those who do wrong. Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga, ndipo sasintha chimene wanena. Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa, komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
3 The Egyptians are men and not God; their horses are flesh and not spirit. When our Father stretches out his hand, the helper will stumble and the one helped will fall, and together they will all come to an end. Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu; akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu. Yehova akangotambasula dzanja lake, amene amapereka chithandizo adzapunthwa, amene amalandira chithandizocho adzagwa; onsewo adzathera limodzi.
4 For this is what our Father said to me: As a lion or a young lion growls over its prey—and though a band of shepherds is called out against it, it is not terrified by their shouting or intimidated by their noise—so the Father of heaven's armies will come down to fight on Mount Zion and on its height. Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi: “Monga mkango kapena msona wamkango umabangula ukagwira nyama yake, ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo, momwemonso palibe chingaletse Yehova Wamphamvuzonse kubwera kudzatchinjiriza phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
5 Like birds hovering overhead, so the Father of heaven's armies will shield Jerusalem; he will shield and deliver it, he will pass over it and rescue it. Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake, Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu; ndi kumupulumutsa, iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”
6 Return to him from whom the people of Israel have so deeply turned away. Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu.
7 For in that day everyone will reject his idols of silver and his idols of gold, which your own hands have sinfully made for you. Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
8 Then Assyria will fall by a sword that is not man's, and a sword not of mankind will devour him. He will flee before the sword, and his young men will be put to forced labor. “Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu. Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga. Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo adzagwira ntchito yathangata.
9 His stronghold will crumble in terror, and his princes will flee in panic from the battle standard, declares our Father, whose fire is in Zion and whose furnace is in Jerusalem. Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha, ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.” Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni, ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]