Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 32 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Look, a king will reign in righteousness, and rulers will govern with justice. Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo, ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
2 Each will be like a shelter from the wind, a refuge from the storm, like streams of water in a dry place, like the shadow of a great rock in a weary land. Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe, adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu, ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.
3 Then the eyes of those who see will not be closed, and the ears of those who hear will listen. Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka, ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
4 The hasty mind will understand knowledge, and the stammering tongue will speak readily and clearly. Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa, ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
5 No longer will the fool be called noble, nor the scoundrel said to be honorable. Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
6 For the fool speaks foolishness, and his heart plots evil: to practice ungodliness, to speak lies about our Father, to leave the hungry with nothing and to deprive the thirsty of drink. Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru, amaganiza kuchita zoyipa: Iye amachita zoyipira Mulungu, ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova; anjala sawapatsa chakudya ndipo aludzu sawapatsa madzi.
7 The scoundrel's weapons are evil; he devises wicked schemes to destroy the poor with lying words, even when the needy pleads his case justly. Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso, iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa. Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
8 But the noble person plans noble things, and by noble things he stands. Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino, Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.
9 You complacent women, rise up and hear my voice; you carefree daughters, listen to what I say. Khalani maso, inu akazi amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji ndipo imvani mawu anga. Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
10 "In little more than a year you will tremble, you carefree women, for the grape harvest will fail, and there will be no gathering. Pakapita chaka ndi masiku pangʼono inu akazi amatama mudzanjenjemera; chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika ndipo zipatso sizidzaoneka.
11 Tremble, you complacent ones; shudder, you carefree ones! Strip yourselves bare and put mourning clothes around your waists. Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu; ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu. Vulani zovala zanu, ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
12 Beat your breasts for the pleasant fields, for the fruitful vine, Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde, ndi mphesa yawonongeka.
13 for the land of my people, where thorns and briers grow up; indeed, for all the houses of joy in the jubilant city. Mʼdziko la anthu anga mwamera minga ndi mkandankhuku. Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
14 For the palace will be abandoned, the bustling city deserted; the hill and the watchtower will become bare places forever, a delight for wild donkeys, a pasture for flocks, Nyumba yaufumu idzasiyidwa, mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu; malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya. Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
15 until the Spirit of our Father is poured out on us from on high, and the wilderness becomes a fruitful field, and the fruitful field is regarded as a forest. Yehova adzatipatsa mzimu wake, ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde, ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
16 Then justice will dwell in the wilderness, and righteousness will remain in the fruitful field. Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
17 The work of righteousness will be peace, and the result of righteousness, quietness and security forever. Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo; zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
18 My people will dwell in a peaceful home, in secure dwellings, in undisturbed resting places. Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere, mʼnyumba zodalirika, ndi malo osatekeseka a mpumulo.
19 Though hail flattens the forest and the city is completely leveled, Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
20 blessed are you who sow beside all the waters, who let the ox and the donkey range freely." inutu mudzakhala odalitsika ndithu. Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse, ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]