Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 33 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Woe to you, destroyer, who have not been destroyed; you betrayer, whom no one has betrayed! When you have finished destroying, you will be destroyed; when you stop betraying, you will be betrayed. Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe, amene sunawonongedwepo! Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri, iwe amene sunanyengedwepo! Iwe ukadzaleka kuwononga, udzawonongedwa, ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga, ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.
2 Our Father, be gracious to us; we wait for you. Be our strength every morning, our salvation in the time of trouble. Inu Yehova, mutikomere mtima ife; tikulakalaka Inu. Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu, ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
3 At the thunder of your voice the peoples flee; when you rise up, the nations scatter. Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa; pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
4 Your plunder is gathered as the locust gathers; like swarming locusts, people rush upon it. Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe. Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.
5 Our Father is exalted, for he dwells on high; he has filled Zion with justice and righteousness. Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
6 He will be the sure foundation of your times, a wealth of salvation, wisdom, and knowledge; the fear of our Father is Zion's treasure. Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu, adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka; kuopa Yehova ngati madalitso.
7 Look, their brave men cry out in the streets; the envoys of peace weep bitterly. Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu; akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.
8 The highways lie deserted; travelers have vanished from the road. The covenant is broken, its cities are despised, no one is respected. Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu, mʼmisewu mulibe anthu a paulendo. Mdaniyo ndi wosasunga pangano. Iye amanyoza mboni. Palibe kulemekezana.
9 The land mourns and wastes away; Lebanon is ashamed and withers; Sharon has become like the desert, and Bashan and Carmel shake off their leaves. Dziko likulira ndipo likunka likutha. Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota. Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala. Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.
10 "Now I will arise,' says our Father, 'now I will be exalted, now I will lift myself up. Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga, ndipo ndidzakwezedwa.
11 You conceive chaff, you give birth to stubble; your breath is a fire that will consume you. Zolingalira zanu nʼzachabechabe ngati udzu wamanyowa. Mpweya wamoto udzakupserezani.
12 The peoples will be burned to ash, like thorns cut down and set ablaze. Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza; ndi ngati minga yodulidwa.”
13 Hear, you who are far off, what I have done; and you who are near, acknowledge my might.'" Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita; inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga
14 The sinners in Zion are terrified; trembling grips the godless: "Who among us can live with the consuming fire? Who among us can live with everlasting flames?" Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha; anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera: Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa? Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
15 The one who walks righteously and speaks what is right, who rejects gain from extortion and keeps his hand from taking a bribe, who stops his ears to plots of bloodshed and shuts his eyes to evil, Angathe kuti ndi amene amachita zolungama ndi kuyankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu, amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.
16 this is the one who will dwell on the heights, whose refuge will be the mountain fortresses; his bread will be given to him, and his water will not fail. Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja, kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri. Azidzalandira chakudya chake ndipo madzi sadzamusowa.
17 Your eyes will see the king in his beauty; they will see a land that stretches far away. Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
18 Your heart will ponder the former terror: "Where is the one who counted? Where is the one who weighed the tribute? Where is the one who counted the towers?" Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija: “Ali kuti mkulu wa Asilikali uja? Ali kuti wokhometsa misonkho uja? Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
19 You will no longer see those insolent people, a people whose speech is too strange to follow, stammering in a tongue you cannot understand. Simudzawaonanso anthu odzikuza aja, anthu aja achiyankhulo chosadziwika, chachilendo ndi chosamveka.
20 Look at Zion, the city of our appointed feasts! Your eyes will see Jerusalem, a peaceful home, a tent that will not be moved, whose stakes will never be pulled up and whose cords will never break. Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu; maso anu adzaona Yerusalemu, mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa, zikhomo zake sizidzazulidwa, kapena zingwe zake kuduka.
21 But there our Father in his majesty will be for us a place of broad rivers and streams, where no galley with oars can go and no mighty ship can pass. Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu. Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo, sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
22 For our Father is our judge, our Father is our lawgiver, our Father is our king; he will save us. Pakuti Yehova ndi woweruza wathu, Yehova ndiye wotilamulira, Yehova ndiye mfumu yathu; ndipo ndiye amene adzatipulumutse.
23 Your rigging hangs loose: it cannot hold the mast in place or keep the sail spread. Then an abundance of plunder will be divided, and even the lame will carry off the spoil. Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka, sizikutha kulimbitsa mlongoti wake, matanga ake sakutheka kutambasuka. Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
24 And no one living in Zion will say, "I am sick"; the people who dwell there will have their sin forgiven. Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala” ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]