Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Hosea 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Say to your brothers, "My People," and to your sisters, "Shown Mercy." “Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’ ”
2 Plead with your mother, plead—for she is not my wife, and I am not her husband—that she put away her whoring from her face and her unfaithfulness from between her breasts, “Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo, pakuti si mkazi wanga, ndipo ine sindine mwamuna wake. Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake, ndi kusakhulupirika pa mawere ake.
3 or I will strip her bare and leave her as naked as the day she was born; I will make her like a wilderness, turn her into a parched land, and let her die of thirst. Akapanda kutero ndidzamuvula, ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa; ndidzamuwumitsa ngati chipululu, adzakhala ngati dziko lopanda madzi, ndi kumupha ndi ludzu.
4 I will show her children no compassion, for they are the children of whoring. Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake, chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere.
5 Their mother has prostituted herself; she who carried them acted in shame. She said, "I will chase after my lovers, who give me my bread and my water, my wool and my flax, my oil and my drink." Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi. Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga, zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi, ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’
6 Therefore I am about to block her path with thorns; I will wall her in so she cannot find her paths. Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga; ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira.
7 She will chase her lovers but not catch them; she will look for them but not find them. Then she will say, "I will go back to my first husband, for it was better for me then than now." Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza; adzazifunafuna koma sadzazipeza. Pamenepo iye adzati, ‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja, pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’
8 She has not realized that it was I who gave her the grain, the new wine, and the oil, I who lavished silver and gold on her—which they spent on Baal. Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta. Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide, zimene ankapangira mafano a Baala.
9 Therefore I will take back my grain when it ripens and my new wine in its season; I will reclaim my wool and my flax, given to cover her nakedness. “Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola, ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa. Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa, zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.
10 Now I will expose her shame before the eyes of her lovers, and no one will rescue her from my hand. Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche ake pamaso pa zibwenzi zake; palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.
11 I will put an end to all her rejoicing—her festivals, her New Moons, her Sabbaths, all her appointed festivals. Ndidzathetsa zikondwerero zake zonse: zikondwerero zake za chaka ndi chaka, za mwezi watsopano, za pa masiku a Sabata ndi maphwando ake onse a pa masiku okhazikitsidwa.
12 I will lay waste her vines and fig trees, of which she said, "These are my wages that my lovers gave me." I will turn them into a thicket, and the wild animals will devour them. Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu, imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake. Ndidzayisandutsa chithukuluzi, ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.
13 I will hold her accountable for the days she burned offerings to the Baals, when she decked herself with rings and jewelry and chased after her lovers—but me she forgot, declares our Father. Ndidzamulanga chifukwa cha masiku amene anafukiza lubani kwa Abaala; anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali ndipo anathamangira zibwenzi zake, koma Ine anandiyiwala,” akutero Yehova.
14 "Therefore, look, I am going to win her back: I will lead her into the wilderness and speak tenderly to her heart. “Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo; ndidzapita naye ku chipululu ndipo ndidzamuyankhula mwachikondi.
15 There I will give her back her vineyards and make the Valley of Achor a doorway of hope. There she will respond as in the days of her youth, as on the day she came up out of Egypt." Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa, ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo. Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake, monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.
16 On that day, declares our Father, you will call me "my husband," and no longer will you call me "my Baal." “Tsiku limeneli,” Yehova akuti, “udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’ sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’
17 I will remove the names of the Baals from her mouth; never again will they be invoked by name. Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake; sadzatchulanso mayina awo popemphera.
18 On that day I will make a covenant for them with the wild animals, the birds of the sky, and the creatures that move along the ground; I will banish bow and sword and war from the land, so that all may lie down in safety. Tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga. Ndidzachotsa mʼdzikomo uta, lupanga ndi zida zonse zankhondo, kuti onse apumule mwamtendere.
19 I will betroth you to me forever; I will betroth you to me in righteousness and justice, in covenant love and compassion. Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya; ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro, mwachikondi ndi mwachifundo.
20 I will betroth you to me in faithfulness, and you will know your Father. Ndidzakutomera mokhulupirika ndipo udzadziwa Yehova.
21 On that day I will respond, declares our Father—I will respond to the heavens, and they will respond to the earth; “Tsiku limenelo Ine ndidzayankha,” akutero Yehova. “Ndidzayankha mlengalenga pempho lake lofuna mitambo ndipo mvula idzagwa pa dziko lapansi;
22 and the earth will respond to the grain, the new wine, and the oil, and they will respond to Jezreel. ndipo nthaka idzamvera kupempha kwa tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo zidzamvera Yezireeli.
23 I will plant her for myself in the land. I will show mercy to "No Mercy," and I will say to "Not My People," "You are my children"; and they will say, "You are my Father." Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga: ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’ Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’ ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]