Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Habakkuk 3 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Pemphero la Habakuku

1Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti.

2Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu;Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa.Muzichitenso masiku athu ano,masiku athu ano zidziwike;mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.

3Mulungu anabwera kuchokera ku Temani,Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani.SelaUlemerero wake unaphimba mlengalengandipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.

4Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa;kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake,mʼmene anabisamo mphamvu zake.

5Patsogolo pake pankagwa mliri;nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake.

6Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi;anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera.Mapiri okhazikika anagumukandipo zitunda zakalekale zinatitimira.Njira zake ndi zachikhalire.

7Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto,mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.

8Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje?Kodi munakalipira timitsinje?Kodi munapsera mtima nyanjapamene munakwera pa akavalo anundiponso magaleta anu achipulumutso?

9Munasolola uta wanu mʼchimake,munayitanitsa mivi yambiri.SelaMunagawa dziko lapansi ndi mitsinje;

10mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka.Madzi amphamvu anasefukira;nyanja yozama inakokomandipo mafunde ake anakwera kwambiri.

11Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga,pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo,pa kunyezimira kwa mkondo wanu.

12Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali,ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo.

13Munapita kukalanditsa anthu anu,kukapulumutsa wodzozedwa wanu.Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa,munawononga anthu ake onse.Sela

14Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wakepamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa,ankasangalala ngati kuti akudzawonongaosauka amene akubisala.

15Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu,kuvundula madzi amphamvu.

16Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri,milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo;mafupa anga anaguluka,ndipo mawondo anga anawombana.Komabe ndikuyembekezera mofatsa,tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo.

17Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,ndipo mʼminda musatuluke kanthu.Ngakhale nkhosandi ngʼombe zithe mʼkhola,

18komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

19Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga;amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi,amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri.Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]