Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

James 2 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Simdaapatula wandhu

1Achabale wanga yawo mumkhulupilila Ambuye Yesu Kilisito, Ambuye wa ulemelelo, musadapatula wandhu. 2Tikambe kuti mundhu mwina uyo wavalila mbhete ya zaabu ni vivalo vokhadwa walowa pamsonghano wanu, ni pamwepo walowanjho mundhu wausiwa uyo wavala misepe. 3Ngati mupeleka ulemu waukulu kwa mundhu uyo wavala vivalo vabwino, ni kukamba kuti, “Khala pampando wa ulemu pachogolo,” nambho kwa mundhu yujha wausiwa mukamba, “Iwe ima pajha, kapina khala yapa panjhi pa ndhaka pafupi ni myendo yanga,” 4ndekukamba kuti mpatula wandhu pakati panu, ni kukhala wolamula kwa kuganizila kuipa kuti wandhu wina niwofunika kupunda kupitilila anjake.

5Achabale wanga wokondedwa, jhiwani kuti Mnungu waasangha wandhu ausiwa apajhiko lapanjhi mchikhulupi ni kulandila ufumu, uwo wadakamba Mnungu kuti siwapache wandhu yawo amkonda iye. 6Nambho anyiimwe mwapepula wandhu ausiwa! Bwanji, osati wandhu wopata ndeyawo akudidimizani anyiimwe? Bwanji, osati wopatawo nde yawo akupelekani anyiimwe kubwalo la nyumba ya milandu? 7Anyiiwo ndeyawo alitukwana jina labwino kupunda la Yesu, uyo anyimwe ni wandhu wake.

8Simuchite bwino kupunda ngati simulivele thauko la Ufumu, ilo liphezeka mumalembo ya Mnungu, nilikamba kuti, “Mkonde mnjako ngati umo ujhikondela umwenewake.” 9Nambho ngati mwapatula wandhu ndande yamaonekedwe yawo, ndekuti mulakwa, ni thauko likuchitani anyiimwe kuti wochimwa. 10Uyo wakana kuvela thauko limojhi siwakhale wakana kuvela matauko yonjhe. 11Pakuti uyo wadakamba kuti, “Usadachita chigololo,” ndeuyo wadakambanjho, “Siudapha.” Ata ngati simudachite chigololo, nambho kupha mukupha, ndekuti mwalakwila mathauko yonjhe. 12Chimwecho mukambe ni kuchita ngati wandhu yawo mujhiwa kuti simulamulidwe kwa thauko ilo litichita kuti tikhale afulu. 13Pakuti Mnungu siwakhala ni lisungu yapo siwamlamule mundhu uyo walijhe lisungu. Lisungu lili ni mbhavu kupitilila lamulo.

Kukhulupilila ni kuchita

14Achabale wanga, kuli phindu lanji ngati mundhu wakamba kuti wali ni chikhulupi nambho siwalangiza kwa vichito kuti wakhulupila? Bwanji, chikhulupi ngati chimecho chikhoza kumupulumucha? 15Ganizilani kuti mbale wakhale wammuna kapina wamkazi, walibe chovala kapina chakudya. 16Sithangatile chiyani ngati anyiimwe kwakambila anyiiwo, “Mnungu wakupache mwawi! Nikupembhelani mkaothe moto ni kukhuta!” Popande kwapacha vofunika vao? 17Chimwecho, chikhulupi icho chilibe vichito chafa.

18Mundhu mwina wakhoza kukamba, “Iwe uli ni chikhulupi, ine nili nivichito!” Yangho langa ni ili, “Nilangize umo mundhu wakhalila ni chikhulupi popande vichito. Nane sinikulangize chikhulupi changa kwa vichito.” 19Bwanji, mukhulupilila kuti kuli Mnungu mmojhipe? Muchita bwino! Nambho ata viwanda vikhulupilila chimwecho, ni kutenthemela kwa mandha. 20Mundhu wopusa iwe! Bwanji, ufuna kulangizidwa kuti chikhulupi chopande vichito vabwino ilibe mate? 21Bwanji, Ibulahimu, nyakubala wathu siwadavomelezedwe ni Mnungu ndande ya vichito vake? Iye wadampeleka mwana wake Isaka pa guwa la mahoka. 22Chimwecho chikhulupi chake ni vichito vake vabwino vidayenda pamojhi, ni chikhulupi chake chioneka kuti cha zene ndande ya njhito zake zabwino. 23Kwakupitila yameneyo, malembo ya Mnungu yadakhala yazene, pokamba, “Ibulahimu wadamkhulupilila Mnungu, ni kwa chikhulupi chake wadavomelezeka kukhala mundhu wovomelezeka kwa Mnungu.” Ndande imeneyo, Ibulahimu wadatanidwa bwenji wa Mnungu. 24Chimwecho mundhu wavomelezeka kukhala wabwino ndande ya vichito vake vabwino, osati ndande ya chikhulupi chokhape.

25Chinchijhanjho kwa Lahabu yujha hule. Iye wadaikidwa kukhala ovomelezeka ndande ya kwaathangatila afukufuku aku Izilaeli yawo wadaalandila kukhomo kwake, ni kwathawiza kwa njila ina. 26Pakuti, ngati umo lili thupi popande mpuyo lafa, nchichijha chikhulupi popande vichito chafa.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]