1Kalata iyi ichokela kwa ine Yakobo, uyo nili mtumiki wa Mnungu ni wa Ambuye Yesu Kilisito. Nikulembelani anyiimwe mafuko khumi ni yawili ya ku jhiko la Izilaeli yawo mwamwazika kumalo yosiyanasiyana ya jhiko la panjhi! Ine nikulonjelani.
Njelu ni hekima
2Achabale, muone kuti ni chimwemwe yapo zifika nyengo za mavuto ni mayeselo yosiyanasiyana,3pakuti mujhiwa kuti kukhulupilila kwanu yapo kuyesedwa, kukuchitani mkhale wolimba mtima.4Mujhiwe zenedi kuti kulimbamtima kwanu sikukuchiteni muyendekele kumkhulupilila Mnugnu mbaka pothela, ni simkhoze kukhala ngati mujha wafunila Mnungu ni chikhulupi chanu chikhale ni mbhavu, popande kuchepekedwa ni kandhu.5Ngati pakati panu pali mundhu uyo wachepekela malango, wafunika wampembhe Mnungu, uyo siwampache mundhu mmeneyo pakuti Mnungu wampacha mundhu waliyonjhe kwa kuchuluka ni ubwino.6Nambho yapo wampembha Mnungu, wafunika kumkhulupilila kupunda popande kumkhaikila. Pakuti mundhu uyo wakhaikila wali ngati mafunde ya nyanja, yayo yavunduka ni kuponyedwa kutali ni mbhepo.7Mundhu uyo wali chimwecho siwadaganiza kuti wakhoza kulandila kandhu kuchokela kwa Ambuye ndande ya kukhaikila kwake.8Pakuti mundhu mmeneyo wakaikila ni wali wa maganizo yawili, siwakhazikika pa vindhu vonjhe ivo wavichita.
Usiwa ni kupata
9Mundhu wamkhulupilila Yesu uyo wali wausiwa wafunika kukondwela, pajha Mnungu wamkweza.10Nambho wandhu amkhulupilila Yesu yawo ali wopata afunika kujhichicha yapo Mnungu wamchicha, pakuti wopata siasowe ngati maduwa yakuthengo.11Pakuti jhuwa liwala, ni kutendha kwake kuumicha mimela, ni maduwa yammela umenewo yakugwa panjhi. Chimwechonjho, wandhu wopata siayomwe yapo achita njhito zawo.
Mayeso
12Ali ni mwawi wandhu yawo ayendekela kumkhulupilila Mnungu ata yapo yakujha mayeso. Anyiiwo sialandile mwawi kuchokela kwa Mnungu ngati salangize kuti amkhulupilila iye. Mnungu siwapache mbhaso ya umoyo wa kukhala pamojhi ni iye, ngati umo wadakambila kwa wandhu yawo amkonda kuti siwapache.13Mayeso yakajha kwako, yakhoza kukupangicha kuchita chindhu choipa. Chimwwecho usakambe kuti, “Mnungu waniyesa kuti nichite vindhu voipa.” Palibe icho chikhoza kumuchita Mnungu kupanga vindhu voipa. Pakuti Mnungu siwampangicha mundhu kuti wachite vindhu voipa.14Nambho kila mundhu wayesedwa kwa kuguzidwa ni kunyengedwa ni khumbilo lake loipa.15Khumbilo loipa limenelo yapo liloledwa kumchoghoza mundhu limchita mundhu wachite machimo, ni machimo yameneyo yakaendekela yamchita mundhu mmeneyo wamwalile.
16Achabale wanga wokondedwa, wasadakunyengani mundhu waliyonjhe!17Mkumbukile mbhaso iliyonjhe ni chindhu chabwino, vichokela kumwamba kwa Mnungu. Iye siwang'anamuka.18Kwakukonda kwake mwene wadati sangha ni kukhala wanawake kupitila uthenga wake wa uzene, kuti tikhale wandhu olemekezeka kupunda kupitilila vindhu vonjhe ivo vaumbidwa.
Kuvela ni kuchita
19Achabale wanga wokondedwa, kumbukilani kuti waliyonjhe wafunika kuvela mwamsanga, ni kuganiza yapo wafuna kukamba, ni siwafunika kukwiya msanga.20Pukuti mundhu wambhwayi siwakhoza kuchita vindhu vabwino ivo wavifuna Mnungu.21Chimwecho, siyani kuchita vichito vonjhe voipa ni ukhalo woipa uwo muchita kila ndhawi. Mufunika mujhichiche ni kulandila Uthenga Wabwino uwo Mnungu wayika mmitima yanu, uwo ukhoza kukuombolani.
22Simudakhala akungovechelape mawu ya Mnungu, nambho chitani chijha mawu yakamba.23Mundhu waliyonjhe wavechela mawu limenelo, walingati mundhu uyo wajhipenya nghope yake pa chiyoo,24wakamaliza kujhipenya ni kuchoka, kwa ndhawi yochepa waiwala umo iwonekela nghope yake.25Nambho mundhu uyo walisunga bwino thauko la Mnungu lakwanila ilo lapacha wandhu ufulu, ni kuyendekela kuligwila thauko asati kuvelape nikuiwala, mundhu mmeneyo siwapachidwe mwawi kwa kila chindhu icho wachichita.
26Ngati pali mundhu mwina wajhichita kuti wali ni dini, nambho walepela kulichekeleza lilime lake kukamba voipa, dini yake ilibe mate ni wajhinyenga mwenewake.27Dini ya uzene ni yovomelezeka kwa Mnungu ni iyi, kwathangatila wana amasiye ni wachikazi afedwa nachamunao pa mavuto yawo, ni kujhilonda ni machimo ya jhiko lino.
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved. Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]
Read offline
Save NTNYBL2025 on this device and read it with no connection. Downloads stay in this browser or app only.