Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 13 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Kumkwadilicha Mnungu

1Mwendekele kukondana ngati umo ifunikila kwa wandhu yawo amkhulupilila Kilisito. 2Simdaiwalila kwalandila alendo, pakuti pakuchita chimwecho wandhu ambili adalandila atumiki akumwamba a Mnungu popande kujhiwa. 3Mwakumbukile wajha amangidwa mndende, mchite ngati mwamangidwa pamojhi nawo. Mwakumbukile anyiwajha avutika mchite ngati mvutika mwaonjhe pamojhi.

4Ukwati ufunika ulemekezedwe ni wandhu wonjhe, nwammuna ni wamkazi afunika akhale okhulupilika, pakuti Mnungu siwalamule wandhu wonjhe yawo achita chigololo.

5Simdakhala wandhu wokonda ndalama, mgwamike ni vindhu muli navo. Mnungu mwene wakamba kuti, “Sinikusiya ni sinikutaya.” 6Ndendande tikhoza kukamba kwa kuchimikiza kuti,“Ambuye nde mthandizo wanga,siniopa.Mundhu siwanichite chiyani?”

7Akumbukileni achogoleli wanu yawo adakulalikilani mawu ya Mnungu. Ganizilani umo amakhalila muukhalo wao, chatani chikhulupi chao. 8Yesu Kilisito siwang'anamuka ni yuyujha jhulo, lelo ni ata muyaya. 9Msadanyengeka ni mayaluzo yayo siyalingana ni Uthenga wa Bwino. Ubwino wa Mnungu nde uwo uchita mizimu yathu ikhale nganganga ni osati thauko la chakudya. Thauko limenelo silidamthangatile mundhu waliyonjhe uyo wadaligwila.

10Ife tilinalo guwa lochochela njhembe ilo ata ajhukulu achita njhito pa nyumba ya kulambila ya ayahudi saloledwa kudya vindhu icho vachochedwa pa guwa limenelo. 11Mchipangano cha kale, mjhukulu wamkulu watenga mwazi wa chinyama ni kulowa nawo pamalo poyela kupunda, ni kuuchocha mahoka ndande ya machimo. Nambho nyama za zinyama zimenezo zibuchidwa pabwalo la mujhi. 12Chinchijha Yesu nayo, wadavutichidwa ni kuphedwa kubwalo kwa mujhi, dala wachite wandhu avomelezedwe ni Mnungu kwa mwazi wake. 13Chipano timpitile kumeneko kubwalo kwa mujhi ni tivomele kulenga njhoni ngati umo iye wadalengela njhoni. 14Pakuti pano pajhiko tilibe mujhi uwo ukhala muyaya, nambho tiulindilila mujhi ujha ukujha. 15Chimwecho chipano, tiyendekele kumtamanda Mnungu kwa kupitila Yesu. matamando yameneyo ningati mahoka yachochedwa kwa milomo ikamba iye nimbuye wathu. 16Simdasiya kuchita vindhu vabwino ni kuthangatilana, pakuti izi nde njhembe izo zimkwadilicha Mnungu.

17Mwavele achogoleli wanu ni kuchata chijha akukambilani, pakuti anyiiwo asunga mizimu yanu usiku ni usana. Ni anyiiwo sakambilile umo adachitila njhito yawo pachogolo pa Mnungu. Mkaavela sachite njhito yawo kwa chikondwelo. Nambho ngati simchita chimwecho sachite kwa chisoni, niimeneyo siikhala ni phindhu kwanu.

18Mtipembhelele ni ife. Ife tichimikiza kuti mitima sitilamula ngati tachita cholakwa chilichonjhe, pakuti tifuna kuchita vindhu vabwino. 19Nikumbembhani kupunda mnipembhele, dala Mnungu wanibweze kwanu chisanga.

Mapembhelo yomalizila

20Mnungu wamuhyukicha Mbuye wathu Yesu Kilisito, uyo wali owesa wamkulu wa mbelele ndande ya kumwaza mwazi wake uwo uchimikiza chipangano cha muyaya. 21Mnungu, uyo wakupachani mtendele wakupacheni kila chindhu chabwino icho mchifuna, dala mkhoze kuchita yajha yonjhe wayafuna, ni kuti wachite mkati mwathu yajha yamkwadilicha mwene kwa kupitila Yesu Kilisito. Ulemelelo ukhale kwaiye, muyaya ni muyaya! Ikhale chimwecho.

Mawu yomalizila

22Chipano anyaabale, nikupembhani mlandile kwa kutonda uthenga uno wa kukuthilani mtima. Ino ni kalata yochepape iyo nakulembelani. 23Nikonda kukujhiwichani kuti mbale wathu Timotheo wathomasulidwa mujha mndende. Ngati wakajha chisanga sinijhe naye yapo sinijhe kwanu.

24Mwalonjele achogoleli wanu wonjhe pamojhi ni wandhu yawo amkhulupilila Mnungu! Abale amkhulupilila Kilisito a ku Italia akulonjelani. 25Nikupembhelani kuti ubwino wa Mnungu uendekele kukhala pamojhi namwe.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]