Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 12 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Mnungu ni Tate wathu

1Ife tilinalo gulu lalikulu la wandhu alangiza kuti akhala kwa kumkhulupilila Mnungu. Chipano tisiye kila chindhu icho chitichekeleza, ni kusiya machimo yajha yatigwililila, chimwecho tijhitaidi kuchita yajha Mnungu wakila pachogolo pathu, ngati umo mundhu watamangila pamasowelo ya liwilo kwa kulimba mtima. 2Chipano timpenyecheche Yesu uyo wadayambicha chikhulupi chathu ni uyo siwachikwaniche. Iye uyo ndande ya chikondwelo chidaikidwa pachogolo pake, iye wadalimba mtima mtanda popande kuganizila njhoni ya nyifa imeneyo, niiye wakhala malo ya ulemu ya Mnungu.

3Ganizilani vindhu ivo vidampata Yesu, ni umo wadalimbila mtima kuchuchidwa ni wandhu amachimo. Chipano msadafa mtima ni msidaleka kumkhulupilila Mnugnu. 4Ingakhale mjhitaidi kuyakhoza machimo, ata chimwecho mkali simdabulane nghondo mpaka kumwaza mwazi wanu. 5Bwanji, mwayawalila yajha mawu yothilamtima yayo Mnungu wakutanani anyiimwe kuti ni wana wake?“Mwanawanga siudadelela kuonyedwa ni Ambuye,siudafa mtima yapo akuonya.

6Pakuti Ambuye amlanga kila mundhu uyo amkonda,ni amlanga kila mundu uyo amvomela kukhala mwana wao.”

7Limbilani mtima chilango ndande ya kuyaluzidwa ni Mnungu. Mnungu wakuchitilani anyiimwe ngati wana wake, pakuti ni mwana yuti uyo siwalangidwa ni obala wake? 8Nambho ngati simlangidwa ngati wana wina, basi anyiimwe osati wanawake wenewene, nambho niwana akumbuyo. 9Pamojhi ni yameneyo ife talemekeza obala wathu, ata yapo atilanga. Chipano tifunika kuvela kupunda Mnungu Tate wathu uwo wali kumwamba dala tikhoze kukhala. 10Obala wathu pano pajhiko adatilanga kwa ndhawi, ngati umo adafunila achina wene, nambho Mnungu watilanga ndande ya phindhu lathu tachinawene, dala tipate kukhala pamojhi niiye ni tikhale woyela ngati umo wali iye. 11Kulangidwa osati chindhu chokondwelecha nambho ni chindhu chodandaulicha. Nambho anyiwaja ayaluzidwa kukhala ni ulemu pothela pake siapate mbhaso ya mtendele kuchoka muukhalo wa bwino.

Kuyaluzidwa ni kuonyedwa

12Chipano thilani mbhavu manja yanu yolenda ni muyathile mbhavu maombono yanu yayo yafooka. 13Yendekelani kuyenda munjila yoongoka, dala wajha afooka alamichidwe ni kuthilidwa mbhavu.

14Mjhitaidi kukhala kwa mtendele ni wandhu wonjhe ni mkhale ukhalo uwo siukuchiteni mvomelezeke ni Mnungu, pakuti palibe mundhu uyo siwamuone Mnungu popande kukhala ni ukhalo ngati umenewo. 15Mjhipenyelele kupunda mundhu waliyonjhe wasadajha kukosa kuchitilidwa vabwino ni Mnungu. Mjhipenyelele dala wasadajha kuchokela mundhu mkati mwanu, uyo wali ngati mtengo wowawa ni kwaapa ambili kwa sumu yake. 16Mjhipemyelele dala pakati panu pasidakalapo ni mundhu wachigololo. Kapina mundhu uyo siwamlemekeza Mnungu ngati Esau, wadagulicha ukulu wake woyamba kubadwa kwa chakudya cha ndhawi imojhipe. 17Anyiimwe mjhiwa kuti ata yapo wadafuna atate wake ampache mwawi kuchokana niiye kukhala mbadwa woyamba, siidakhozekane pakuti siwadapatenjho malo yolapa, ata ngati wadafunafuna kwa misozi.

18Anyiimwe simdafike ku phili la Sinai ilo likhoza kugwilidwa, ni ilo limakwelela moto ni mtambo wa kuda ni mdima waukulu ni mbhepo yaikulu ngati umo adachitila wandhu ajhiko la Izilaeli, 19kudachokela mvekelo wa mbetete ni mvekelo uwo ukamba mawu yoofya. Yawo adavela mvekelo umenewo adapembha asadavelanjho mawu lina, 20pakuti sadakhoze kuimila nganganga lamulo ilo lidachochedwa, “Chalichonjhe sichigafye pili ili sichibulidwe myala, ata ngati chinyama.” 21Yameneyo yonjhe yadachokela kuphili la Sinai yadaofya kupunda wandhu, ata Musa wadakamba, “Nitendhemela kwa mandha.”

22Nambho anyiimwe mwafika pa phili la Sayuni, pa mujhi wa Yelusalemu ya kumwamba kwa Mnungu, umenewo ni mujhi wa Mnungu uyo wali wamoyo. Umo atumiki ambili akumwamba a Mnungu akomana. 23Mwafika pa msonghano waukulu wa ubadwa oyamba wa Mnungu, yawo maina yawo yalembedwa kumwamba kwa Mnungu. Muima pachogolo pa Mnungu wali mlamuli wa wandhu wonjhe, ni pachogolo pa mizimu ya wandhu achita vabwino yawo achitidwa kukhala okwanila. 24Mwafika kwa Yesu uyo wali ovanichana muchipangano cha chipano, ni uyo mwazi wake uwo udamwazika ukamba vindhu vabwino kusiyana ni ujha ya Abeli.

25Chipano mjhipenyelele msadajha kukana kumvechela mmeneyo wakamba nianyiimwe. Ngati anyiwajha adakana kumvela yujha adawaonya pano pajhiko ni sadaomboke, bwanji ife tikhoze bwanji kuomboka ngati tikana kumvechela yujha wationya kuchokela kumwamba? 26Ndhawi ijha Mnungu wadakamba paphili la Sinai mvekelo wake udatendhemecha jhiko, nambho saino wakamba kuti, “Sinitendhemechenjho jhiko, nambho osati jhikope, sinitendhemeche ni kumwamba kumlengalenga.” 27Mawu limenelo, “Nalonjho” litilangiza kuti vindhu vonjhe vaumbidwa sivitendhemechedwe ni sivikhalapo dala vikhalile vijha sivitendhemechedwa.

28Ife nafe, tiyamike pakuti tilandila ufumu uwo siutingizika. Timuyamike ni kumlambila Mnungu kwa mtundhu uwo umkwadilicha ni kukhala ni ulemu pachogolo pake, 29pakuti Mnungu wathu wali ngati moto wokalipa uwo uyomwecha.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]