Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 11 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Kumkhulupilila Mnungu

1Chikhulupi ni kusia kukhaikila kuti Mnungu siwatipache vindhu ivo tiviembekeza, ni kuchimikiza kuti vindhu ivo sitiviona chipano nivazenedi. 2Pakuti azee wathu adavomelezedwa ni Mnungu ndande ya chikhulupi chao.

3Kwa chikhulupi ife tijhiwa kuti jhiko lidaumbidwa kwa mawu la Mnungu, vindhu vioneka vidaumbidwa kuchokana ni vindhu ivo sivioneka.

4Kwa chikhulupi Abeli wadamchochela Mnungu mahoka yadali yabwino kupitilila yajha wadachocha Kaini. Kwa chikhulupi chake wadavomeledwa ni Mnungu kuti wachita yavomelezeka, Mnungu mwene wadazivomela njhembe zake. Kwa chikhulupi chake ingakhale wadafa, wakali kukamba.

5Kwa chikhulupi Enoki wadatengedwa ni Mnungu, kuchoka pajhiko siwadamwalila. Siwadaonekenjho ndande Mnungu wadamtenga kupita kumwamba kwa iye. Malembo yakamba kuti yapo wadaliwakali osatengedwe, iye mamachita yayo yamkwadilicha Mnungu. 6Chimwecho popande chikhulupi siikhozekana kumkwadilicha Mnungu. Pakuti mundhu waliyonjhe uyo wamchata Mnungu wafunika wakhulupilile kuti Mnungu walipo, nikuti wapacha mbhaso wajha amfunafuna kumjhiwa iye.

7Kwachikhulupi Nuhu wadaonyedwa ni Mnungu kwa nghani ya vindhu va pambuyo ivo vidali sividachokele. Wadamvela Mnungu, wadamanga ijha Safina iyo wadalamichidwa iye pamojhi ni wandhu amnyumba mwake. Kuchokana ni yameneyo jhiko lidalamulidwa. Niiye Mnungu wadavomela kuti Nuhu wachita yajha yayoyavomelezeka pachogholo pake.

8Kwa chikhulupi Ibulahimu wadamvela Mnungu yapo wadatanidwa wapite kujhiko ilo Mnungu wadakampacha likhale lake, wadasamuka mjhiko lake ingakhale siwamajhiwe uko wamapita. 9Kwachikhulupi Ibulahimu wadakhala ngati mlendo kujhiko wadakambidwa ni Mnungu kuti siwapachidwe, wadakhala kumeneko muhema ngati umo adakhalila Isaka ni Yakobo, yawo adapata chinchijha ngati umo wadakamba Mnungu kuti siwapache Ibulahimu. 10Pakuti Ibulahimu wamalindilila mujhi uwo uli ni msingi wolimba, mujhi uwo Mnungu mwene wadaupanga ni kuumanga. 11Kwachikhulupi Ibulahimu ata ngati wadali mzee kupunda, wadalandila mbhavu za kukhala tate ata ngati Sala siwamabale ndande ibulahimu wadakhulupilila kuti Mnungu siwampache icho wadamkambila. 12Ibulahimu wadali mzee kupunda ngati mundhu wakufa, nambho kupitila kwa mundhu mmeneyo mmojhi, wadapata mibadwa yambili iyo siiwelengeka ngati ndhondwa ni mchenga wa pamtunda.

13Wandhu yawa wonjhe adamwalila uku ali ni chikhulupi. Adamwalila akali sadalandile vindhu ivo Mnungu wadaakambila kuti siwapache, nambho kwa kutali adaviona, adakondwela ni kuvomela kuti anyiiwo adali alendo ni wandhu alibe pokhala pano pajhiko. 14Wandhu yawo akamba vindhu ngati vimenevo, alangiza kuti alifunafuna jhiko lawo wene. 15Ngati amakaliganizila jhiko ilo adachoka kale, adakakoza kubwelanjho kumeneko. 16Nambho pambuyo pake adayembekeza jhiko lili labwino kupunda, nde jhiko la kumwamba kwa Mnungu. Ndendande Mnungu siwaona njhoni akamtana iye ni Mnungu wao, ndande iye mwene wathokwakonjela mujhi.

17Kwa chikhulupi Ibulahimu wadamchocha mahoka mwana wake Isaka ndhawi ijha Mnungu wadamuyesa. Mmeneyo Ibulahimu ndeuyo wadakambidwa ni Mnungu kuti siwapachidwe mwana, ata chimwecho wadavomela kumchocha mahoka mwana mmeneyo wayoka, 18ata ngati Mnungu wadamkambila kuti, “Siupate mbadwa kupitila Isaka.” 19Ibulahimu wadakhulupilila kuti Mnungu wakhoza kwahyukicha akufa, tikhoza kukamba zenedi Ibulahimu wadampatanjho mwana wake uyo wadali ngati wamwalila.

20Kwa chikhulupi Isaka wadaapacha mwawi Yakobo ni Isau, wapate mwawi uwo ukujha pambuyo.

21Kwa chikhulupi Yakobo yapo wadali pafupi kumwalila, wadapacha mwawi wana wonjhe wa Yusufu, wadamlambila Mnungu uku ni wakwatamicha mutu wake pa mpulu wake.

22Kwa chikulupi Yusufu yapo wadawandikila kumwalila, wadakamba nghani za Aizilaeli kuchoka kwa ku jhiko la misili, ni wadaasiila maagizo kwa nghani za vifupa vake.

23Kwachikulupi obala Amusa adambisa mwana mmeneyo kwa ndhawi ya myezi itatu yapo wadabadwa. Adamuona kuti ni mwana wabwino, chimwecho sadaliope lamulo la mfumu.

24Kwachikhulupi Musa yapowadakula, wadakana kutanidwa mwana wa mwali wa Falao. 25Wadaona mbasa kuvutika pamojhi ni wandhu Amnungu, kusiyana ni kukondwela machimo kwa ndhawi yochepa. 26Wadajhiwa kuti kuvutika ndande ya Kilisito ni kwabwino kupunda kupitilila kupata konjhe kwa jhiko la Misili, pakuti wamapenyelela mbhaso yapambuyo.

27Kwa chikhulupi Musa wadachoka kujhiko la Misili popande kuopa mbwayi ya mfumu, ni siwadabwelele mmbuyo, pakuti wadali ngati yujha mundhu wamwona Mnungu uyo siwaoneka kwa maso. 28Kwachikhulupi Msa wadachita phwando la Pasaka, wadalamula mwazi unyunyuzidwe pamwamba pa vicheko, dala yujha mtumiki wa kumwamba a Mnungu wapeleka nyifa, siwadaayomwecha mbadwa wa jhiko la Izilaeli.

29Kwa chikhulupi wandhu ajhiko la Izilaeli adayomboka nyanja ya mchele ya Shamu ngati pamtunda. Nambho wandhu ajhiko la Misili yapo adayesa kuchita chimwecho adafela mmajhi.

30Kwachikhulupi wandhu a Izililaeli adazizungulila mapupa ya mujhi wa Yeliko kwa siku saba nazo zidagwa. 31Kwachikhulupi Lahabu uyo wadali hule siwadayomwe pamojhi ni anyiwajha adampanduka Mnungu, ndande wadaalandila anyiwajha akafukufuku.

32Chipano nikambe chiyani kupunda? Pakuti ndhawi siinilola kukamba nghani za Gidioni ni Balaki ni Samsoni ni Yefisa ni Daudi ni Samweli ni alosi. 33Kwachikhulupi yawa wonjhe adabulana nghondo ni mafumu ni adakhoza. Adachita vindhu vovomelezeka, ni adalandila vijha wadaakambila Mnungu kuti siwapache. Adacheka makamwa ya mikango, 34adathima malilime yokalipa ya myoto, adapulumuka kupedwa ni maupanga, adali ofooka nambho adapata mbhavu. Adali ni mbhavu munghondo, adaakhoza obula nghondo achilendo. 35Kwachikhulupi wachikazi adabwezeledwa wandhu wao yawo adahyukichidwa pambuyo pa kumwalila. Wina wao adakana kumsiya Mnungu kuti akhale ufulu, chimwecho adavutichidwa mpaka kumwalila dala apate kuhyukichidwa ni kulowa muumoyo wabwino kupunda.

36Wina adanyozedwa ni kubulidwa mikwapulo, ni wina adamangidwa minyololo ni kuikidwa mndende. 37Wina adabulidwa myala, adadulidwa vipinjilivipinjili, ni kuphedwa kwa maupanga. Wina adazungulila zungulila uku avala vikwetu mbelele ni vikwetu va mbuzi, adali wandhu osauka, adavutichidwa ni kulandidwa. 38Jhiko la panjhi silidafunike kukhala ni wandhu abwino ngati anyiyawa. Amazungulilazungulila mnghalambo ni mmaphili, amakhala mmayenje ni mbhanga.

39Wandhu anyiyawa wonjhe adamkwadilicha Mnungu ndande ya chikhulupi chawo. Atachimwecho sadalandile vindhu vijha Mnungu wadakamba kuti siwapache, 40pakuti Mnungu wadathotiikila ife chindhu chabwino kupunda, dala ife pamojhi ni anyiiwo tilandile yajha wadakamba kuti siwatipache.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]