Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 10 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Pakuti thauko ni chitunjhipe cha vindhu vabwino, asati wenewene wa vindhu vene. Ndande ino siikhozeka kwa kupitila mahoka yayo yachochedwa chaka mbaka chaka, kwachita ivo sivijhe ni siyakhoza kumchita mundhu wasiye machimo! 2Ngati wandhu amenewo amlambila Mnungu adakali alekeleledwa machimo yao ni kuchitidwa zenedi kukhala Amnungu, sadajhivelanjho kuti ali ni machimo ni mahoka yameneyo yonjhe yadakatha. 3Nambho mahoka yameneyo yachitika kila chaka, dala kukumbuchila wandhu machimo yawo. 4Pakuti mwazi wa mbhongo wa ng'ombe ni mbuzi sivikhozelatu kuchocha machimo ya wandhu.

5Ndendande Kilisito yapo wadajha pano pajhiko, wadamkambila Mnungu,“Siudafune mahoka kapina njhembe,nambho wanikonjela thupi dala nilichoche kwako.

6Iwe siukwadilichidwa ni njhembe zopyeleza,kapina njhembe zochocha machimo.

7Pamenepo nidakamba kuti,‘Nilipano najha, ngati umo yalembedwela muchikalakala cha thauko,imwe Amnungu najha kuchita yajha yakukwadilichani.’”

8Poyamba wadakamba, “Siudafune ni siudakwadilichidwe ni mahoka ni njhembe zopyeleza ni njhembe za kuchocha machimo.” Wadakamba chimwechi ata ngati njhembe izi zonjhe zimachochedwa kuchokana ni thauko. 9Niwadakambanjho, “Nili pano, imwe Amnungu najhikonja kuchita icho mfuna.” Chimwecho Mnungu wadachocha mahoka ya kale ni pamalo pake Mnungu wadamwiika njhembe imojhipe nde Kilisito. 10Pakuti Yesu Kilisito wadachita ngati umo wafunila Mnungu, ife talekeleledwa machimo yathu ni kuchitidwa kukhala Amnungu kwa mahoka ya thupi lake ilo wadalichocha kamojhipe nikukwana.

11Mjhukulu waliyonjhe yujha Myahudi wachita njhito yake ya kulambila masiku yonjhe, ni kuchocha mahoka yayajha mala zambili, mahoka yayo siyakoza kuchocha machimo. 12Nambho Kilisito wadachocha mahoka mala kamojhi ndande ya machimo. Mahoka yayo yachita njhito sikuzonjhe, ndipo wadakhala malo ya ulemu ya Mnungu, 13wamlindila Mnungu wakhoze adani wake ni kumchita walaamulile. 14Chimwecho kwa hoka lake limojhi, wachita wandhu anyiwajha onjhe alekeleledwa machimo yawo, ni kwachita kukhala Amnungu ni akhale popande kuchita machimo muyaya. 15Niiye mzimu woyela watichikizila kuti ivi ni vazene. Poyamba wadakamba kuti,

16“Ichi nde chipangano icho sinichite nawo masiku yakujha, akamba Ambuye,Siniike thauko langa mmitima mwao,ni kulilemba mmaganizo yawo.”

17Niwakambanjho kuti,“Sinikumbukilanjho machimo yawo,kapina vichito vawo voipa.”

18Chimwecho machimo yonjhe yakathochochedwa, sikukalanjho ni ndande yo chocha mahoka yayo yachocha machimo.

Timuwandikile Mnungu

19Chipano achaabale wanga, kwa mwazi wa Yesu utichita sitidaopa kulowa pamalo papatulidwa ndande ya Mnungu. 20Iye watimasulilila njila ya chipano, njila ya umoyo, kwa kupitila ijha paziya, njila imeneyo ni thupi lake mwene. 21Tilinayo mjhukulu wamkulu kupunda uyo wali ni ulamulilo pa mwamba pa nyumba ya Mnungu. 22Chipano timuwandikile Mnungu kwa mtima wazene ni kuendekela kumkhulupilila, kwa mitima iyo yalekeleledwa nakuochedwa mandha yojhivecha kukhala ni machimo, ni mathupi yayo yachukidwa kwa majhi yabwino. 23Tijhigwilicha kupunda yajha niyakhulupilila ni kuyaembekeza, pakuti Mnungu uyo watikambila kuti siwatipache ni wokhulupilika. 24Tijhisamalana ni kuthangatilana ife kwa ife ni kuthilana mtima dala kulangizana chikondi ni kuchitilana vabwino. 25Sitidasiya lijha khalidwe lopezana pamojhi, ngati mujha wina achitila. Nitifunika kuthilana mtima, pakuti siku lobwela Ambuye lawandikila.

26Ngati tikayendekela kuchita machimo kwa dala, pambuyo pakuujhiwa uzene, palibe mahoka yayo ya khoza kuchochedwanjho dala yachoche machimo. 27Nambho icho chakhalila ni kulindilila kwa mandha lamulo la Mnungu ni moto okalipa uwo siuwayomwoche wonjhe yawo amkana Mnungu. 28Mundhu waliyonjhe uyo siwavela thauko la Musa, wamaphedwa popande lisungu kukakhala ni umboni wa wandhu awili kapina atatu. 29Bwanji, mganiza ni chilango chachikulu cha mtundu wanji icho wafunika wapachidwe mundhu yujha wamdelela mwana wa Mnungu, ni kuudelela mwazi wa chipangano cha Mnungu udamuyelecha mundhu mmeneyo, ni mundhu wamtukwana mzimu Mnungu wafunika wapande chilango cha mtundu wanji? 30Pakuti timjhiwa yujha wadakamba, “Ine sinibwezele mbwezo, ine sinibwezele,” ni wadakambanjho, “Ambuye saalamule wandhu wake.” 31Ni chindhu choofya kupunda kupezana ni lamulo kuchokela kwa Mnungu wali wamoyo!

32Mkumbukile yajha yadachokela siku zijha zoyamba yapo mudamkhulupila Kilisito. Ata ngati siku zijha mdapata mavuto yambili, anyiimwe mdalimba mtima. 33Ndhawi zambili mdatukwanidwa, mdachochedwa ulemu padanga, ndhawi yina mdali tayali kulunjana ni anyiiwajha adavutichidwa mtundhu umwewo. 34Mdaachitila vabwino yawo adamangidwa, niyapo mdalandidwa chuma chanu mdalimba mtima kwa kukondwa, pakuti mdajhiwa kuti muli ni vindhu vabwino vikulindilani ivo vikhala muyaya. 35Chipano simdataiza kupilila kwanu, pakuti sikukupacheni mbhaso yaikulu. 36Ifunika mlimbe mtima dala mkhoze kumkondwelecha Mnungu ni kulandila chijha wadakukambilani kuti siwakupacheni. 37Yalembedwa mmalembo ya Mnungu kuti,“Ikali ndhawi yochepape,ni yujha wakujha siwajhe,ni siwachedwa.

38Nambho mundhu wanga uyo wachita yayo yavomelezeka kwanga, siwakulupilile ni kukhala,nambho wakasiya kunikhulupilila,ine sinikondwelechedwa niiye.”

39Ife sitilimo mkati mwawajha asiya chikhulupililo ni kusowa, nambho ife tili pamojhi ni anyiwajha akhulupilila ni kulamichidwa.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]