Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 9 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Kulambila ngati umo lifunila jhiko ni ngati umo wafunila Mnungu

1Chipangano choyamba chidali ni khalidwe lake lolambila, ni kudali ni pamalo yapo padapatulidwa pano pajhiko ndande ya kumlambila Mnungu. 2Padakonjedwa hema ya Mnungu iyo malo yake yapabwalo yadatanidwa pamalo yapo papatulidwa ndande ya Mnungu. Mmenemo mdali ni kinala cha nyali, guwa ilo lidali ni mabumunda yayo yadachochedwa kwa Mnungu. 3Kumbuyo kwa paziya la kawili padali ni chumba china, icho chidatanidwa pamalo paikidwa ndande ya Mnungupe. 4Mmenemo mdali ni meza iyo idakonjedwa kwa zahabu njhito yake idali ni kubuchila ubani, ni mdali ni bokosi la chipangano, ilo lidanyekedwa zahabu mabendeka yake yonjhe. Mkati mwake mdali ni mphika wa zahabu uwo udali ni chakudya chimatanidwa mana. Kudalinjho ni mpulu wa Aloni uwo udamela machamba, ni vijha vidufya viwili va myala vidalembedwa malamulo ya Mnungu. 5Pamwamba pa bokosi limenelo padali ni viboliboli va voumbidwa viwili ivo vidali ni mapaphiko ivo vilangiza ukulu wa Mnungu, ni mapaphiko yawo yadayenela pamwamba pa chiviniko cha bokosi la chipangano icho chilangiza lisungu. Nambho saino sitikhoza kukamba mokwanila pa nghani za vindhu vimenevo. 6Vindhu vonje vimenevo vidali vathokonjedwa. Uwu udali mwambo wa ajhukulu kulowa kila siku muchumba cha kubwalo cha hema ni kuchita njhito yawo ya ujhukulu. 7Nambho mjhukulu wamkulu yokha nde wamalowa mujha muchumba cha kawili, naye wamachita chimwecho kamojhipe kwa chaka. Wamatenga mwazi wa chinyama uwo wamaupeleka kwa Mnungu ndande ya kuchocha volakwa vake mwene ni volakwa va wandhu wina yawo adachita popande kujhiwa. 8Ndande ya mwambo umenewo Mzimu wa Mnungu utiyaluza padanga kuti pajha lijha hema la pabwalo likali landoima, njila yolowela pamalo yapo patulidwa ndande ya Mnungu idali ikali siidamasulidwe. 9Chindhu ichi ni chifani cha ndhawi za chipano, ilangiza kuti njhembe ni mahoka ya zinyama yachochedwa kwa Mnungu, nambho sizikhoza kuichita mitima ya wandhu amlambila Mnungu kukhala yoyela. 10Nambho yaya yonjhe yakambilila nghani za vakudya ni vakumwa ni makalidwe yosiyanasiyana yosamba. Yaya yonjhe ni maagizo yakubwalope, yameneyo yonjhe yadata pajha Mnungu yapo siwang'anamule vindhu vonjhe kukhala vachipano.

11Nambho Kilisito wajha dala wakhale Mjhukulu wamkulu wa vindhu vabwino ivo sazino vathofika. Iye ndeuyo wachita njhito muhema lina ilo lili labwino kupunda, kupitilila lijha loyamba ilo silidamangidwe ni wandhu. Hema limenelo osati lajhiko lino. 12Iye wadalowa pamalo poyela mala kamojhipe, uku ni watenga mwazi asati wambuzi kapina wa mbhongo wa ng'ombe, nambho wadatenga mwazi wake mwene, ni kutipacha uwomboli wa muyaya. 13Wandhu yawo samavomelezedwe pa kumlambila Mnungu, adavomelezeka kumlambila Mnungu, kwa kunyunyuzilidwa mwazi wa mbuzi ni wa ng'ombe pamojhi ni vyoso va ndama. 14Nambho kwa mwazi wa Kilisito, vindhu vavikulu kupunda vichitika. Kwa mbhavu za mzimu wa muyaya Kilisito wadajhichocha mwene mahoka yokwanila kwa Mnungu. Mwazi wake siutiyeleche maganizo yathu kuchokana ni vichito vipeleka nyifa, dala tikhoze kumtumikila Mnungu wali wamoyo.

15Chimwecho Kilisito ni ovanichana wa chipangano cha chipano dala anyiwajha adatanidwa ni Mnungu, akhoze kulandila mwawi wa muyaya uwo Mnungu wadakamba kuti siwapache. Nyifa yake yoombola wandhu kuchokela mvolakwa ivo adavichita uku ali panjhi pa chipangano cha kale.

16Ngati umo ili mawu yayo wayakamba mundhu kuti yani wapate malo ya chuma chake, mawu yameneyo siyayamba kuchita njhito pambuyo pa iye kumwalila kuchimikiza kuti iye wamwalila. 17Mawu yameyo siyakhoza kuchita njhito mbaka nyifa ichokele, ndande mawu yameneyo yalibe mate ikhala mundhu uyo wakamba mawu yameneyo wakali wamoyo. 18Ndendande ata chijha chipangano choyamba, sichidachitike popande kumwaza mwazi. 19Poyamba Musa wadauuzila wandhu wonjhe malamulo yonjhe ngati umo yadali muthauko. Wadatenga mwazi wa ndama pamojhi ni majhi, ni kwa kutumila machamba ya hisopo ni pamba yofuwila, wadanyunyuzila mwazi chijha chikalakala cha thauko pamojhi ni wandhu wonjhe. 20Musa wadakamba kuti, “Uno ni mwazi uchimikiza chipangano mudalamulidwa ni Mnungu, mchivele.” 21Chinchijha, Musa wadamwazila mwazi ujha muhema ya Mnungu ni vindhu ivo vidatumilidwa pakumlambila Mnungu. 22Zenedi thauko lifuna chimwechi, vindhu vonjhe vikhoza kuchitidwa vivomeleke ni Mnungu kwa mwazi, ni machimo yakhoza kuchochedwape pajha mwazi umwazika.

Kilisito lihoka ilo lichocha machimo ya wandhu

23Vindhu vimenevo ni chifani cha zene kumwamba, vadafunika kuchitidwa kukhala va Mnungu kwa mtundu umenewo. Nambho vindhu va kumwamba vifuna mahoka yabwino kupunda. 24Pakuti Kilisito siwadalowe pamalo yapo pa patulidwa ni Mnungu yapo pamangidwa kwa manja ya wandhu, malo yameneyo ni chifanipe cha malo yauzene. Iye wadalowa pamalo pa patulidwa ndande ya Mnungu yokha poyela kupunda, uko saino watipembhela pachogolo pa Mnungu. 25Mjhukulu wa mkulu wa Ayahudi walowa pamalo papatulidwa ndande ya Mnungu yokha mala kamojhi pachaka, uku wali ni mwazi wa chinyama. Kilisito siwadalowe kumwamba kwa Mnungu mala za mbili nambho wadajhichocha njhembhe kamojhipe. 26Ngati idakakala chimwecho, Kilisito wadakavutichidwa mala zambili kuyambila kuumbidwa kwa jhiko. Nambho ndhawi zino yapo ziwandikila mathelo yake, iye wachokela kamohjipe kuchocha machimo ya wandhu kwa kujhichocha mwene wake mahoka. 27Chimwecho ngati mujha mundhu waikidwa kumwalila kamojhipe nikuima pachogolo pa lamulo la Mnungu, 28mchimwecho Kilisito naye wadajhichocha mahoka mala kamojhipe ndande ya kuyachocha machimo ya wandhu ambili, yapo siwachokele kakawili. Osati ndande ya kutenga machimo, nambho ndande ya kwalamicha wajha amlindila kwa khumbilo.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]