Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 3 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Yesu ni wamkulu kupitilila Musa

1Anyabale wanga wandhu a Mnungu yawo mwatanidwa ni Mnungu, ganizilani nghani za Yesu mtumwi ni mjhukulu wamkulu wa yajha tiyakamba kuti tiyakhulupilila. 2Iye wadali wokhulupilika kwa Mnungu, uyo wadamsangha wachite njhito yake ngati mujha Musa wadali wokhulupilika kwa wandhu wonjhe anyumba ya Mnungu. 3Yesu wafunika wapate ulemu waukulu kupitilila Musa, pakuti uyo wamanga nyumba walemekezedwa kupunda kupitilila nyumba yene. 4Pakuti nyumba yaliyonje ijha imangidwa ni mundhu, nambho Mnungu ndeuyo wamanga vindhu vonjhe. 5Musa wadali mtumiki wokhulupilika pa kwachogoza wandhu wonjhe anyumba ya Mnungu, niwadakamba vindhu ivo Mnungu siwavikambe pambuyo. 6Nambho kilisito ni mwana wokhulupilika uyo wali ni ulamulilo pamwamba pa wandhu anyumba ya Mnungu. Ife tawene ni wandhu wake ngati tikaendekela kukhala nganganga ni olimba mtima kwachijha tichiyembekeza.

Kupumulila uko Mnungu siwapache wandhu wake

7Chimwecho, ngati umo Mzimu wa Mnungu ukambila,“Lelo ngati mkavela mvekelo wake,

8simdakhala osavela ngati ndhawi ijha mdanipandukapandhawi ijha ya mayeso kuphululu.

9Kumeneko kuphululu azee wanu danichucha ni kuniyesa dala achione icho sinachite,ata ngati adaviona vichito vanga kwa vyaka alobaini!

10ndande imeneyo nidaakwiila wandhu amenewo, nane nidakamba kuti,‘Wandhu anyiawa akana kunichata,niakana kuchita yajha nakambila.’

11Chimwecho nidakwiya ni kulumbila,‘Salowelatu pajhiko ilo dikaapacha dala apumulile.’”

12Chipano abale jhipenyeleleni pasadajha kukhala ni mundhu waliyonjhe pakati panu uyo wali ni mtima woipa, niuyo siwakhulupilila ni kujhipatula ni Mnungu wali wamoyo. 13Nambo mfunika mtangatilane mwachinawene kwa mwachinawene kila siku ilo litanidwa lelo, dala pasakhalepo ata mmojhi wanu uyo wakhoza kunyengedwa ni machimo, ni kukana kumkhulupilila Mnungu. 14Ife tigwilizana ni Kilisito ngati tikayendekela kumkhulupilila Mnungu ngati mujha tidakhulupilila kuyambila mmayambo mbaka pothela, pamenepo sitikhale pamojhi ni Kilisito.

15Yalembedwa chimwechi mmalembo,“Ngati mkavela mvekelo wake lelo,msidaichita mitima yanu kukhla yolimbangati mujha azee wanu akale amakana kuchogozedwa niine.”

16Niachiyani adauvela mvekelo wa Mnungu ni kukana kuchogozedwa niiye? Niwajha wonjhe adachogozedwa ni Musa kuchokela ku kujhiko la Misili. 17Mnungu waadakwiila achiyani kwa vyaka alobaini? Wadakwiila wajha adachita machimo, adamwalila ni vitanda vawo vidali vambili kujha kunghalambo. 18Mnungu yapo wadalumbila, “Sialowa pamalo panga popumulila,” pamenepo wamakambila achiyani? Wamaakambila wajha adakana kumvela. 19Chimwecho tiona kuti sadalowe kumeneko ndande ya kosakhulupilile kwao.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]