Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 2 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Uwomboli wodabwicha

1Chimwecho tifunika kujhipenyelela kwa nghani ya uzene ujha tidauvela, dala tisidajha kuyasiya. 2Uthenga ujha azee wathu adapachidwa niatumiki akumwamba Amnungu, udalangizidwa kuti ni wauzene, ni mundhu waliyonjhe uyo siwadauchate ni kuuvela, wadalangidwa ngati umo idafunikila. 3Chipano ife sitiomboledwe bwanji ngati sitisamala uwomboli wodabwicha mtundu uno? Ambuye wene nde adali woyamba kuuzila uwomboli uno, nianyiwajha adamvela adatichimikizila kuti ni vazene. 4Mnungu wadachimikiza yameneyo kwa kuchita vodabwicha ni vozizwicha vambili, kwa kwagawila wandhu mbhaso ya mzimu wa wake ngati umo wadafunila mwene.

Uyo watichogoza pa uwomboli

5Mnungu siwadaike atumiki akumwamba alamulile jhiko ilo likujha, ilo tikambilila nghani zake. 6Niatachimwecho pamalo pina malembo yakamba kuti,“Mundhu ni chindhu chanjhi mbaka umganizile?Iye ni yani mbaka umsamale?

7Kwa ndhawi yochepape udamchita kukhala panjhi pa atumiki Amnungu akumwamba,wamveka chisoti cha ukulu ni ulemelelo,

8ni udamchita walamulile vindhu vonjhe.”Ikambidwanjho kuti Mnungu wadachita mundhu kukhala ulamulila wa vindhu vonjhe, popande kuchisiya ata chimojhi. Hata chimwecho chipano, sitimuona mundhu niwavilamulila vindhu vonjhe.

9Nambho timuona Yesu uyo kwa ndhawi yochepape wadachitidwa kukhala panjhi kupitilila Atumiki akumwamba Amnungu, dala kwa ubwino wa Mnungu wamwalile ndande ya wandhu wonjhe. Chipano, timuona Mnungu wampacha ukulu ni ulemelelo ndande ya nyifa iyo wadavutichidwa. 10Idamkwadilicha Mnungu uyo wadaumba vindhu vonjhe ni kuviika umo vili ni kumchita Yesu uyo wali chiyambo cha uomboli kukhala ngati umo wafunila iye kwa kupitila kuvutika. Wadachita chimwecho dala Yesu waombole wandhu ambili ni kwalovya kuulemelelo wake.

11Yesu waadachita wandhu achameneo akhale wandhu Amnungu, iye pamojhi ni wandhu ameneo wonjhe ali ni atate amojhi. Ndendande Yesu siwaona njhoni kwatana achamenewo abale wake. 12Yesu wadakamba kuti,“Imwe Amnungu sinaakambile abale wanga vichito vanu.Sinikutamandeni pa msonghano wao.”

13Niwakambanjho,“Chikhulupi changa sinichiike kwa Mnungu.”Nchimwecho,“Ine nilipano niwana yawo wanipacha Mnungu.”

14Chipano wana amenewo ngati umo waatanila, niwandhu ali ni thupi ni mwazi. Yesu mwene wadali ngati amenewo ni wadagwilizana ni umundhu wawo. Wadachita chimwecho dala panjila ya nyifa yake, wamuyomweche satana uyo wali ni mbhavu ichiticha wandhu amwalile, 15dala wapache ufulu wandhu adali akapolo ndande ya kuopa nyifa pa umoyo wawo wonjhe. 16Pakuti ijhiwika kuti iye siwadajhe kwatangatila atumiki akumwamba Amnungu, nambho wadajha kwathangatila wandhu amibadwa ya Ibulahimu. 17Ndande imeneyo wadafunika wakhale ngati achabale wake pa kila mtundu, dala wapate kukhala mjhukulu wamkulu wali ni lisungu ni uyo wachita ngati umo ifunikila pa kumtumikila Mnungu, dala kwakupitila iye Mnungu wakhoze kwalekelelela wandhu machimo yawo. 18Iye wakhoza kwathangatila wajha ayesedwa, pakuti iye mwene wadavutichidwa ni kuyesedwa.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]